Namadingo ayenda ulendo wa ndawala

47

Atadzipereka yekha kusaka ndalama kuthandizira odwala cancer pogwiritsa ntchito luso lomwe namalenga adamupatsa, m’modzi mwa oyimba nyimbo za uzimu Petience Namadingo tsopano wamaliza zonse.

Malingana ndi Namadingo iye wati tsopano wapseda zonse lero pa 24 May 2017 ndipo ndalama zonse zomwe wapeza kudzera kuyimba nyimbo imodzi pa nthawi kwa akufuna kwabwino, akazipereka ku chipatala chachikulu cha Queen Elizabeth Central ku Blantyre.

Patience Namadingo Malawi Music

Namadingo akufuna kuthandiza odwala.

Namadingo yemwe adatchuka kwambiri ndi nyimbo yake ya ‘Mtendere’ adakonza malingaliro opeza ndalama zokwana 1.2 miliyoni mu masiku 40 kudzera kuyimba nyimbo imodzi kwa amene wamuyitana ndipo amayenera kulipira 3,000 kwacha koma iye adakakamizika kukweza ndalamazi kufika pa 5 miloyoni malinga ndi m’mene chikoka chidakwerera pa lingaliro la Namadingo.

Pogwiritsa ntchiyo Gitala imodzi, nyimbo imodzi, ndi oyimba m’modzi, oyimbayu wakwanitsa kupeza ndalama zokwana 11 miliyoni mu masiku 40, kutsatila anthu ndi ma kampane omwe akhala akuthandiza pa malingalirowa zomwe iye wati zamukondweretsa kwambiri.

Mmalingana ndi oyimbayu ndalama zokwana 11,520, 000 zapezeka kudzera mu dongosololi.

Namadingo wapempha aMalawi ambiri kukapezeka pamene iye akakhale akutula cheke cha ndalamazi ku QECH ponena kuti chithuchi achipanga ndi iwo eni.

Pa tsiku lomwe iye walitcha kuti ‘La40 lakwana’wakonzanso ma T-shirt olembedwa ‘La40 lakwana’ kuti anthu avale pamene akuyenda ulendo wa ndawala kukasiya ndalamazi.

“Tikhala ndi mwambo wa pamwamba kwambiri kuchokera pa bwalo Kamuzu upper kupita ku QECH kukapereka cheke choyerekeza cha ndalama zokwana K11 520 000. Tachipanga chithuchi tonse tsono tiyeni tichimalizenso tonse” adalongosola Namadingo.

“Tikugwirana manja ndi ndi a chipatalachi posankha iwo amene apereke zipangizo zomwe zikifunika. Nditengere mwayi uwu kuthokoza aMalawi onse pothandiza chinthuchi sindikuzitenga zophweka ndithu” adawonjezera m’mawu ake.

Oyimbayu wakhala akuyenda malo osiyanasiyana monga m’makomo, m’maofesi, ndi m’makampani kuyimba nyimbo pompo pompo ndi gitala yake mcholinga chofuna kuthandiza ku wodi ya cancer ya ana ku QECH.

Share.

47 Comments

 1. zkomo ambuye tkukwezan tikuyamikani polenga namadingo ndkumpasa nzelu kut athandize osowa,amasiye,okalamba ndso ovutika mzosez tkuti zikomo mlungu wamphamvu zonse mlandile ulem ndmatamando kuchoka kumwamba mdaliseso namadingo ambuye akudalisen namadingo mpitilize kuthandza ovutika ndiosowa

 2. Ndimaganizo abwino kwambiri c hifukwa cancer yavuta heavy.I wish God to bless him when he anticipates to make that journey not only that, but also to collect alot of money from people.

 3. Great Almighty GOD bless you day buy day…..zikukanika eni achumawa ndalama kukasunga kunjan pomwe ma millions a amalawi akumwalila kusowa ndipanado yemwe……mulungu akupatseni moyo wautali

 4. ᵀʰᶦˢ ᶦˢ ˢᵒ ˢᵐᵃᶫᶫ ᵗᵒ ʳᵉᵃᵈ ᵉᵛᵉᶰ ᶠᵒʳ ʸᵒᵘ ᵇʳᵒ⋅

  ᴰᵒᶰᵗ ᵗʳʸ ᵗᵒ ᶜᵒᶰᵗᶦᶰᵘᵉ ʳᵉᵃᵈᶦᶰᵍ ᵗʰᶦˢ ᵇᵉᶜᵃᵘˢᵉ ʸᵒᵘʳ ᵉʸᵉˢ ʷᶦᶫᶫ ˢᵗᵃʳᵗ ᵗᵒ ʰᵘʳᵗ ˢᵒᵒᶰ ᶦᶠ ʸᵒᵘ ᵈᵒᶰᵗ ˢᵗᵒᵖ⋅

  ᵂʰʸ ᵈᵒᶰᵗ ʸᵒᵘ ˢᵗᵒᵖ﹖⋅⋅⋅⋅ᵍᵒ ᵃʷᵃʸ ᵇʳᵒ ᵃᶰᵈ ʳᵉᵃᵈ ᵗʰᵉ ᶰᵉˣᵗ ᶜᵒᵐᵐᵉᶰᵗ⋅ˢᵗᵒᵖ ʳᵉᵃᵈᶦᶰᵍ ᵃᶫʳᵉᵃᵈʸ﹗

  ᴵ ˢᵉᵉ ᵗʰᵃᵗ ʸᵒᵘ ᵈᵒᶰᵗ ʷᵃᶰᶰᵃ ᵍᶦᵛᵉ ᵘᵖ ʳᵉᵃᵈᶦᶰᵍ⋅⋅⋅ʷᵉᶫᶫ ᵒᵏ, ʸᵒᵘ ʷᵒᶰ ᵗʰᶦˢ ᵗᶦᵐᵉ,ᵇᵘᵗ ʸᵒᵘ ˢʰᵒᵘᶫᵈ ᵍᶦᵛᵉ ᵐᵉ ᵃ ᶫᶦᵏᵉ ᶠᵒʳ ʷᵃˢᵗᶦᶰᵍ ʸᵒᵘʳ ᵗᶦᵐᵉ.

 5. Mene mnyamatayu akupeleka zonse zomwe ali nazo, ma mp akugawana ma lap top odula heavy. Palibe wa opposition wakana lap top. Shee! Ndiye azitinamiza

 6. Uku NDE kuganiza! Osangongoti kuganiza chabe kma kuchita za mzeru! Pomwe RNA akufuna kut matumba awo adzadze mpakana mzikwamwa mwao NDE adzathandize anzawo! Ndipomwe anthu ngat namadingo akuchita! Ndikukhulupila out ambuye ndi amend atachite kwakukulu ice ndi ongoyamikira bax!

%d bloggers like this: