“Hallo! Ndi kumwamba kumeneko…ndilankhu­leko ndi Mulungu,” m’busa alankhulana ndi Mulungu pa selefoni

Advertisement
Pastor Paul Sanyangore

Masiku otsiliza mudzaona zinthu zosiyanasiya zina zoona komanso zina zomusemera Mulungu koma iye asananene kalikonse mkamwa make, malemba amatero mu buku lopatulika.

Izi zikupherezera pamene m’busa wina m’dziko la Zimbabwe akuti walumikizana ndi mulungu osati mu pemphero koma pa foni yake ya m’manja.

Pastor Paul Sanyangore
Abusa Paul Sanyangore kulankulana ndi Malungu pa lamya.

Mmalingana ndi ka vidiyo kamene Malawi24 yawona, kakuonetsa m’busayu yemwe dzina lake ndi  Paul Sanyangore mpingo wa victory world international ministries akuti akulankhulana ndi mulungu pa foni pamaso pa khwimbi la wanthu mkachisi.

Ka vidiyoka komwe kawanda kwambiri pa masamba a mchezo pofika lolemba pa 22 March kadali katawonedwa ndi anthu okwana mazana 77 pa tsamba la mchezo lija lotchedwa You tube. Ndipo kakuonetsa m’busayu ali ndi mzimayi ovala zovala zoyera ali kutsogolo manja ake ali okweza atagwada pamaso pa m’busayu.

M’busayu akumveka ndi kuoneka akumufunsa Mulungu kuti alankhule chani kwa mzimayi yemwe wagwada pa patsogolo pake ndipo waoneka akumvetsera modekha kusonyeza kuti wina akuyankhulana naye pa foni yake ya mmanjayo.

“Halloo! Kodi ndi kumwamba kumeneko?, kodi ndiyankhulenji kwa mzimayi amene ndili naye panoyu?” (Hello, is this heven? I have a woman here, what do you have to say about her) Adafunsa m’busa pa foni pake.

Mpingo onse mosakhulupilira ukuoneka ozizwa komanso idabwa kwambiri ndi zomwe m’busayu wachita. Pamene mnyamata wina akumveka akuyankhula mozimuka kuti “oooh Mulungu alemekezeke”

Povomereza zoyankhulidwa pa foni, Paul wamveka akuvomereza kuti “ooh ok ndimufunse kuti Sibo ndi ndani?” Anayankhula m’busayu.

Atafunsa iye kuti Sibo ndi ndani? anaoneka akulankhulanso pa foni kumufunsa uyo amayankhula nayeyo kuti anene chinachani mzimayiyu, ndipo anamufunsa mzimayiyu kuti “mchifukwa chiyani
Akundionetsa mtima” ndipo ziyankha za mzimayiyu sizinamveke popeza amayankha monong’ona.

Mulungu akuti tipempherere ana ako onse awiri, akuti m’modzi ndi odwala khunyu ndipo wina ndi wa matenda obanika kupuma” (he says we should pray for your children, two of them, he is saying one is epileptic the other one is asthmatic) adauzidwa mzimayi.

Anthu ambiri a mumpingiwu awoneka akusangalala kutamanda mtumikiyu pochita zodabwitsa kulankhulana ndi mulungu pa telefoni ndipo analankhula mwa thamo kuti kumwamba kukupezeka pa foni (heaven is here) ndipo anauza mzimayiyu kuti nyengo zake zasintha.

Komabe izi zadzetsa mafunso ambiri ndipo anthu enanso a mu mpingowu sakukhulupirira kuti izi mzowona.

Advertisement

135 Comments

 1. The worst still to come. But they shall be expose. Kuyamwa mabele,cucumber, drink petrol,doom, lot of stupid funny things. And the worst part ladies are taken so fast because they are desperate for marriage and money. If they join they say they are born again and ali ndimakani koopsa. Mudzalangidwa

 2. Kkkkk padziko lapasi,, zochitika mbwee,, ngat zilichomcho nde bwez tikuyakhulana ndachina malemu Bingu muthalika,, kamuzu banda,, vic Marley,, matafale

 3. Koma munthu ukadya ndikukhuta Osama mphatikiza Mulungu ukamafuna kulankhula Chifukwa tembelelo lake limakhala loopsya kwambili tamvana!!!!

 4. Mmmh guys take it easy, i hope you don’t know who this guy is, he is a comedian not a prophet kk search his name or bio on google. its drama kk

 5. These days u black people u had know money. ur are going to dstry the Earth. White ppl thera quite. It’s really real that black one thy are not created in the emage of God. If you are emage of God why you are playing with him

 6. Mwina upangiri uwu mudachitapo anzanganu Chim Exodus Dante Kaunda Yung Jay Päùl Schwéigèr Nèwå Victor Nthutha Phiri Gule Enangu Rombeziz

  1. haha ine ndimangodziwa kut #Paul analowa kusiling,i mkumauza m,dala wake kut amugawile gawo lake lachuma,..m,dala posaziwa kut nd paul ali musiling,i ati amkaona ngt nd Mulungu akumulankhula

 7. Ananena Kale Yesu Alah Salamu MTendele Ndimadali Amulungu Ankhale Pa Iye, Kt Matsiku Omaliza Kuzabwera Aneneli Onyenga Namanenela Mudzina Langa Namat Alikuno Yes Musamukeko, Km Lero Ndizomvesa Chison Kwabas Tingoti Tikamva Kt Kwabwera Proft Anthu Komko Koma Tisamale Ndi Aneneri Onyengawa Alemelera Painu

 8. kkkkk kodi pano mulunguyo mukumamutenga changa juice wamalambe? motomoto kwanonse omutengera mulungu kokamuyensa

 9. Osamangoti ku zimbabwe apa muzinena ndi maina omwe azibusawo ndi madela ake. Kumangoti akuti akuti kumeneko m’busa wina. Akuti yo ndi ndani?

 10. Koma Ku Zimbabwe Ku nchiyani wina posachedwa pompa waima poyera ndimati iye ndi Mulungu wina nkumati ayende pamadzi wadyedwa uyu ndiye aziti wayankhula ndi Mulungu nchiyani koma Ku zim

 11. Koma tikakhala tisamamutenge MULUNGU kukhala chopepuka ngat momwe tingachezele ndi abale kapen azizathu bcz mulungu ali ekha.Ndpo tizizivela chisoni chifukwa cha zonse zomwe amatipangila zaulere Tizasowa chowilingula

 12. Kkkkkkkkk bodza ili ndi waonjedza bola anzake ametenga sing’anga kumapanga za masenga kunamizila Mulungu .zikuwayendala mpaka kugula ndege koma uyu aliyense akungoziwilatu kuti ndiwabidza ndi ma South Africa omwe anthu ongikhulupilila zilizonse koma zimenezo sangakhulupilile hahaha .

 13. Ndiye pofunika tafunse kuti atigayileko # number ya mulungu yo nafenso tayimbire asamangoyimba okha ayi. Nafenso tidandauleko za mavuto ali padziko panowa. Mwina angatikhululukire

 14. Hallo,Hallo God…. Can you hear me?
  I’m a pastor,from Zimbabwe am calling on behalf of the church…. Hallo…. Halloooooo eish…
  Net work yavuta.
  exodus 20:7.do not use my name for evil purposes….. (Forgive him lord for he don’t know what he is doing)

 15. Thus Why muno mu zambia anawakaniza ku bweramo aneneli onyengawa pamodzi ndi bushiri koma anaopyeza kuti iye bushiri azapha yemwe anamkaniza kulowa mu dzikoli la zambia.

 16. Azathu achikhilisitu ndiye mwaonjeza kwambiri kaya kukhata mondokwa kaya ndi chamba ndiye muziona mpaka kuyakhula ndi Mulungu pa cellphone koma yaaa ziliko

 17. Koma ano masiku otsiriza.maso muli nao koma simuona, makutu muli nao koma simuva.wandituma ine yesu kuti ndiuuze mpingo wake udziwerenga mau amulungu usasochere njira yake:patie Namadingo

 18. Ooo I don’t hv more words to say but what kind of this madness ?is he thinks that all we don,t know the Bible ?wrong business sorry

 19. Panopa Kupempha Kudzera Mupemphero Zatha Pano Ndi Pompo Pompo Clear Clear Pa Phone Kumvana Akane Akane ,alore Alore Alore Kkkkkk Pano Ndie Ziri Pa Easy Kuphwekeratu Ali Ndi No, Yake Andigaileko Pliz Ku Inbox Ndilankhule Naye Ameneyu

 20. koma izi ndiye iiiiiiih anawonjeza kaya mwina iyeyo …….prophets are doing those things to attract more followers so that chopeleka chizikhala chambiri #business as usual .

Comments are closed.