Ikakuona litsiro mvula sikata pofuna kukuchititsa gombe kuti uwonekere ng’amba ku wanthu kuti ndiwe wa umve. Izi zikufanana ndi zomwe zikuchitikira timu yayikulu ya Nyasa Big Bullets.
Mwambiwu ukulumana mapiko kwambiri ndi timu ya Bullets zomwe zitsekule maso kuti penapake pali vuto ku timu yayikuluyi.
Mavuto a kusachita bwino kwa Bullets ayangata ndi kumanga nthenje pamene zavundukuka kuti chiyambireni chaka cha mpira cha 2017 Bullets yavutika ndi kusosoledwa dzitsukwa mu masewero aliwonse.

Chachikulu chachitika pamene timuyi yasenzetsedwa akatundu awo onse ndi kutulutsidwa mu chikho cha ma timu asanu ndi atatu a m’dziko muno cha Airtel.
Kuyambira tsiku limene bungwe loyendetsa masewero a mpira wa miyendo m’dziko muno la Football Association of Malawi (FAM) lidatsekulira chaka cha masewero mu 2017, timu ya Bullets yomwe idatenga chikho cha ligi chaka cha 2015 sidapambanepo masewero aliwonse.
Timuyi koyamba idatherana zilo kwa zilo pamene idasewera ndi Chitipa United mu chikho cha TNM, masewero awo a chiwiri adasewera ndi Silver Strikers pa bwalo la Bingu national sabata latha ndipo iwo adaluza ndi chigoli chimodzi kwa duu. Chigoli cha Silver adagoletsa ndi wosewera wakale wa Bullets Victor Limbani.
Mu masewero omwe iwo atulukira mu chikho cha tsopanochi lamulungu Bullets sidachinyane ndi timu ya Silver pa bwalo la Mulanje kupangitsa iwo kutuluka koma asadachinye chigoli ngakhale chimodzi cheni-chenichi mu chikho cha ndalama za nkhani nkhanichi.
Malingana ndi maganizo a anthu wena, timuyi ikuvutika kwambiri chifukwa ikusowa anyamata a njala kutsogolo pamene iwo a Bullets ati kusapambanaku m’chifukwa cha kuchoka kwa wawo wakale Chiukepo Msowoya yemwe pakali pano akusewera mpira m’dziko la South Africa.
Ena akuti osewera monga Muhammad Sulumba, Bright Munthali ndi Collins Nkhulambe akulephera kukhala ndi ukali, njala, nkhwidzi, chibaba ndi golo ngati m’mene adalili Chiukepo ali ku Nyasa.
Maso a Bullets tsopano ayang’ana chikho chachikulu chokha cha m’dziko muno cha TNM supa ligi pamene asemphana ndi ndalama zokwana 15 miliyoni kwacha kwa owina chikho choseweredwa nthawi yochepachi.
Ma timu a Nyasa Big Bullets, Azam Tigers, Mafco ndi Blue Eagles atuluka mu chikho cha Airtel pamene Mighty Beforward Wanderers, Silver Strikers, Moyale ndi Kamuzu Barracks apitilira mu ndime ina kuyandikira fungo la ndalama zochokera ku kampani ya ma foni a m’manjayi.
60 thoughts on “Bullets yatuluka mu chikho cha Airtel Top 8”
Comments are closed.

Ndiye palivuto ngati
Kkkkkkkk kodi maliro amenewa akulilira kuti? ….neba bola wafika….kkkkk
Kkkkkk komaTeam yanga Bullets, yandimvetsa nyunyunyu.
Yatuluka as if yachita kufuna
yalowa mu top 9 tsopano
Hehede! uluuu! Neba sakumvesa akuwona ngat akulota. Size yako ndi ya mmidzi iwe