Mpira wa kuno ndi mbwelera, angosewela ngati ndado – watelo RVG ponena za Supa Ligi

321

Amene mumagundika kupita ku ma bwalo kumapeto kwa sabata kukaonela mipira ya Ligi ati mwina pena mumakangoonela ndado basi chifukwa mipira ina yakuno ndi yosalongosoka. Pena mwina ukuonela utha kumayesa anthu angosewela ndi ndodo.

RVG

RVG: Mukusewera ndadotu anyamata

Malingana ndi mphunzitsi wa tsopano wa timu ya Flames, Bambo Ronny van Geneugden iwo ati ataonelako pan’gono mipira ya Supa Ligi adziwa kuti mpira wa ku Malawi ndi mphwepwa, panja penipeni.

Malinga ndi malipoti a nyuzipepala, Bambo RVG ati iwo ananena kuti mu ina mwa mipira imene anaonela, anangochoka akupukusa mutu basi kuyesa kuti mwina zimaseweledwa pamenepo zinali ndado osati mpira wa miyendo.

“Ndinene pano kuti ndaonela masewero ena a mu Supa Ligi koma ayi ndithu ndi panja penipeni. Anthu amangodunyula mpira basi, ali nawo ali nawo, wa 12 koloko Nyasalande. Zopanda tsogolo zenizeni,” iwo anatero.

Bamboo RVG ananenanso kuti koma mu masewero ena, zimaoneka kuti tsogolo lilimo ndithu dipo atolamo anyamata ena amene akufuna kukabindikila nawo pokonzekela masewero a mpikisano wa COSAFA.

Share.

321 Comments

 1. Kukhala coach Wa Malawi sichinthu chapafupi…… Get ready to tek the blame iwe akuti ndani kaya.. Rvg…. Kuno ndkumalawi…. Chikhalidwe ndi mpira omwe…..

 2. enanu mumangoxiwa kuonera simungathe kusewera koma kunyoxa basi timu yamalawi ikanakhala kuti ikuwina iyeyo ntchito sakanalembedwa ndimau akewo waxiwikiratu kuti palibe chimene angachite ntchito sakuixiwa kape ameneyo he must fired foseki

 3. Nkulu ameneyu salunama ayi… Ndimaonera game ya Noma ndi Tigers on MBC tv, oh akulu nkhunda zenizeni, or chilakolako cha mpila kukhala ngati akukwawa. Boxing nde eh akumamenyana wina wagwa wina pamwamba… Poor Malawi zambili zotivuta

 4. kufera zakunja muone mmene azidyere ndalama za ku malawi mpira wake sowe vuto ndi osewera mpira samatha basi kuvomereza ndino zinthu zikamakanika osakakamira ntunda opanda madzi,tiyeni tizingokhulana ndi achina chingambwe omwewa basi masiku namapita.

 5. Kusukulu Timapita Kut Tikakumane Ndi Aphunzitsi Omwe Ali Odziwa Ntchito Yao Ncholinga Choti Umbuli wathuwu Uthe So Ngat Tidalemba Ntchito Iyeyo Asatinyoze Ndife Mbuli Tavomela So Tithandizetu Tsopano

 6. Sananame ngakhale pang’ono. Ngati anthu amasowa chowonera Ali mstadium momo. Kuona ma player athu akuthamangathamanga ngati MBAWALA. Koma onenera naye akulongosola zazitsa ndimapesi. Zinthu zinasokonezeka Basi.

 7. koma chimene ndimaziwa ine munthu ngati nkhani kapena chilichonse akungoonapo chofooka chimene munthu ayankhula sitipeza yankho nkhani ndiyoti kodi zimene ayankhulazo ndizoona kapena ayi komanso player aliyese azione kuti akupanga bwanji I think tikhoza kuona kusintha

 8. FAM was supposed to hire a coach who knew the type of football played in Malawi. He is confused now, yet he had promised to deliver.

 9. Kkkkkkkk chiso wanena zoona anawa ndi mfiti za mapiko athakati enieni sadziwa kanthu biiiii, hahaahaaa nkhwezule izi anaming’omba awa

 10. Ngati Iyeyo ali coach wodziwa bwn ntchito, ayikonze kt team yo ikhale yapamwamba. Kuonera Dwangwa Ndiye Kt Wamaliza Ma Team Onse? Asathe Mau!

 11. so if Malawian foot ball is thrush, what is he going to do?. is he going to take players from zambia? a bad carpenter always brames his tools, thats what I know , Kinah Phiri anayesera bwanji kuichinya Egypt ili mu form,, Kape ndi kape, alira ndipo sanati.

 12. Yah but the thing is I blame the FAM president, instead of developing football he and his board members are busy cashgating. So ya kulira tizamlekapo yayi unless the entire board is dissolved. Look at what kinnah did, he took the flames to AFCON ,of which many coaches from outside the country have failed to do. But they continue to hire coaches that doesn’t understand our style.so its better to hire coaches from within the country that understand katchayiro kabola lithu .these problems will never end without dissolving the board. If he also doesn’t want to coach the flames he can go osati kuti walyenge Waka ndalama zithu chaa! Tukhumba maresults yaonekenge.

 13. Coach odziwa azitero mwina zingasintheko.ena mmalo molemba nkhani kuti imveke bwino mukukemba zoziwa nokha ngati ngati chili chidule mukulephera chifukwa maganizo akupelekedwa apawa ndioti anthu ambiri awerenge kuti kodi inuyo mwalemba kuti chani? Nde ngati mukuona kuti chichewa ma sentence ake akumatalika zilembani English alipo omwe analowa mkalasi awerenga ndipo akumvani kuti mukuti chani

 14. Rvg akunena zoona kwathu kumalawi mpira tikulephela.Chikufunika apa kumaprimary sukulu ndikumasecondary sukulu kukhale mipikisano tikatero timu yathu izakhala yamphamvu.

 15. Iyeyu adalembedwa kuti achotse ndado waziwonazo ndiye ndi ntchito yake kuthetsa ndadozo ngati momwe anakonzera Kim zaka zapitazo kuti achina kamwendo adzitchuka

 16. Amalawi tidakhala bwanji kumadabwa mtswamtswa wathu womwe this coach is right kodi unduna wazamasewero umapanga chian?ndizaka zingati achititsako maphunziro aucoach macadamy ampira alipo angati ngati dziko chabwino talimbikitsani masewerawa pa primary level zikuvutaso moti zowona ntchito ingokhala kulimbirana ndalama zapagate mastadium basi please try to improve.

 17. he is employed to change things not to complain,he must implement what he thinks will emprove the current situation,he must come with solutions thats what he is paid for..if everything was fine on the ground he could not find himself there..the officials went as far as looking for acoach outside the country bcoz the knw the problem..go on mr man and do ure job all we need are results and better be good

 18. Wangofuna kupezerapo mwayi team ikamaluza azipeza polankhula kuti azinama kuti paja ndinanena kaletu kuti mpira kuno kulibe,iyeyo ngati wapeza bvuto alikoze team ili mmanja mwake zisamulephere nthaei yomweyi asatinamizepo apa

 19. Ndintchito Yake Coach Kut Akonze Team Yathu Mmene Iye Amkabwera Kuno Mayesa Anazithemba Kut Ndiwoziwa Ntchitoyo,amaganiza Kuti Apeza Team Ili Yoziwa Kale Iye Azingomwa Tea, Ngat Saziwatu Ntchitoyo Basi Go Back To Theway That He Come

 20. He’s right, the system of standard of playing has gone completely down since the generation of like these list of players resigned.

  Andrew chikhosi
  Johns Nkhwazi
  Sherry Msuku
  Gift zakazaka
  Peter Mgangira
  Chancy Vin gondwe
  Chikondi Banda
  Hendrix Banda
  Albert en Bob Mpinganjira
  Wilfred Nyalugwe
  Grant,Lungu etc

  Footbal pano si ili muja moti inkat ikakhara dabby BB n Noma, wina akakachinya uku within aminute wina kukapanga equalise. Lero kulibe now this game full of immature stars so they are diluting the flavour and the taste of the game of football as they do at home Diluting like super dip of wakawaka, Davita or Baks. No sweet soccer. Soccer has been miserably diluted.

  • Amenewo ndi chabe man but the likes of kinnah phiri , jack chamangwana,bernett GONDWE, frank sinalo Kennedy and Holman malunga,damiano malefula,Boniface maganga,donex gondwe,spy msiska, zoro msiska,mavuto lungu, Clifton msiya etc

  • Man Aubry Matenje, inuyodi ndi _1, mumazitsata ndipo mukunena zoona chifukwa mastandard ampirawa akutsikiratsikirabe..
   Chifukwa kagulu ndinatchula kaja nkuthekadi nkotsikadi kusiyana ndi mizwanya mwaitchulayi. Big up Bigman potikumbutsa

 21. The Coach Z Here To Improve The Game Instead Of Working On The Mistake He Has Started Blaming Thats A Bad Carpenter The Cooperate World Too Z To Blame 4 Giving Hm A Free Car Decoder And A Phone Hw Abt Gerald Phiri Senior And Dekilek This Guys Need To B Given Aswell If We Are To Make A Better Flames Coz These Guys Will Not B Happy

 22. RVG wouldnt talk like this in Zimbabwe for sure.This is being very primitive.That is why he was hired inorder to change our national team

 23. He is right za football kwathu kuno ndi phada kapena tinene kuti jingo weni weni and we don’t want to learn from our mistakes hence we continue with the very same blunders . Nanga tikane kuti ndimbwelera mpira wathu?

 24. I dnt think he is right being a coach he wasnt suporse to speak like that bcoz he is like a leader.
  He would have just say he has failled not blaming our league.malawi has good quality and skilled players all we need is to motivate them in all sectors

 25. The best way to solve a problem is to identify some weaknesses that’s what RVG has done cause frankly speaking our nation team is a total disgrace

 26. Ya that’s true, even you Admin, you don’t have even Dstv so that u can see what happening outside your country, to have tv doesn’t mean you have Dstv, let’s start putting Dstv now.

 27. Amalawi tisiye kukhala ndi maganizo oti player weniweni ndi was bullets kapena was wanderers, yafika nthawi sono yoti tiyambe kuona ma player Ama team angono angono

 28. ndiye malawi amene ndimawaziwa ine ameneo tikukukwiya chan apa iye ngat wanena kut mpira wa kuno mw nd phala nde tidikile kut apanga xotan kut tiyambe kuchta bwino imeneyo nd nchito yake iyeyo, nde mungot azipita azipita kut? nanga akunama ngat?

 29. Word RVG. kumatenga dzi ma player dza Super League bola kumakatenga ana a FMB under 20 league at least they play football that has identity. Super League coaches chitamponi kanthu phu phu phu si zampira. Player wa super league kumakanika ndi ball control yomwe?

 30. guys know that truth shall set every body to be free,kunena zoona couch sakunama athoka chilungamo,kumalawi Juno mpila sitimatha,kma chigololo,kachasu,kupondelezedwa,apo NDE tili pa number wani,koma mpila simbaliyathu.

 31. Peter K Nchacha E!Man Mwalankhula Chilungamo Koma Poti Chilungamo Chimapweteka Azingotilalatirabe Basi Sinanga Iye Ndi Mnzungu!Kkkkk Moti Kulankhula Kumeneko RVG Wayankhula APM Ali Kuti!Iiiiiiii Amalawi Ndiye Taphweka Bwanji Ndiwobwela Omwe Mpakana Kumayima Pachulu Hahahahahaha!

 32. kumalawi mpilakulibe or,atabwela morinyu palibechingasinthe.anyamata athuamakondakumwamowa kachasu,ntonjan,akangontchuka pang,onotzibwenzinkat

 33. sakunama mkulu ameneyu,kumangoti nebaneba za ziiiiii,mpira omakoma kumvera pa radio koma kukaonera pamaso zeroooooh weniweni wekhaso kumadabwa kuti olengeza aja amalengeza ziti kodi,kk apanso akuononga mpira ndi olengeza anthuwa amakokomeza za ziii,ali timu mmene ikusewelera omvera tukuuzani ili bwino mxxx zausiru bax

 34. Malawi is good at rewarding mediocrity. This RVG thing has started with losses yet he has been given a car, phone and decoder. What are we promoting?

  • Is RVG a mediocre? in what respect? he brought new tactics and the players he found in camp were not picked by him and were too rigid to put his tactics into practice judge him akasankha squad ya kumtima kwake. chomwe nduona zakuwawani ndi zomwe ampatsazo. but using the word mediocrity on him is unfair and just shows how you dont understand football

 35. Mpira wathu udzapita patsogolo ngati makampani ndi anthu akufuna kwabwino mu dera lanuro akadzayamba kutenga nao gao mu mpira , tiyeni tiyambe kuthandiza mma primary komanso ma secondary school kuti kudzitiluka ma players abwino then tidzaona maligi athu akuchita bwino

 36. Phala lake limaseweredwalo! How can we expect flames to perform well when our superleague is trush. What government must do is to invest on youth talents

 37. uyu ndi coach wa nyamilandu anapeza othandiza kulipira salary ndi iye, ine chomwe ndimadziwa ndichoti ngakhale mutatenga ma coach a Chelsea,man u, barca , arsenal, spurs kukocha Malawi sitingawine ,vuto sima coach koma players ,

 38. Timaziwa kale kuti team yathu ndi mbola,koma akuyenera kuonesa ntchito yake ngati Coach, koma ngati walephera basi azipita,asationongere ndalama

  • Kusula mohwepwa sichinthu chamasewera chimatenga zaka zambiri that’s why kwa anzathu kuli ma academy a mpira koma anthu amasulidwa kuyambira ali mafana …. Super league yinkakoma nthawi yomwe ma teams anali ndi ma youth clubs bcoz zimapangitsa kuti ma first 11 awo akhale ndi madolodi oti akamakankha Chikopa timayamikira kuti zoona sitinabetse dollar koma zinalowa chibwana

 39. Iyeyo Ngat Coach Achita Bwino Kudziwa Mamistake Athu. Ndiye Amanena Kut Timasewera Ndado.Ndado Tingasithe Bwanji? Ndi Ntchito Yake Ya Coach

 40. kwathu kuno kukanakhala kt timadziwa mpira sibwezi ataitanitsa iyeyo iye agwire ntchito yomwe anabwerera kt timuyo isinthe ifikepomwe iye akufunapo ndezomwe tikudikira ife,,

 41. Akunena zoona mkulu ameneyu kwabasi ndiye bolaso pa zambia. Panopa yatumiza under 20 ku world cup chomwe ndi chikho cha achisodzela osapitilira zaka 20

 42. Mmmmm Coach asathe mawu iye wabwera kudzaphunzitsa masewera ampira.Kungoyerekeza Flames kumenyedwa mu Cosafa ameneyu anyamuka basi.

 43. If it is like that just show him the door to go back where he come from. I think the time he was signed acontract with FAM, they told him what he is suppose to do. Ngati kunoko kulibe mpila ndiye amadzataniko?, just fire him before it is too late.

 44. zoona mpira kuno kulibe mungoganiza zija anafuna kupanga sulumba pa bingu stadium kudabukila kugolo kwake chosecho ali pagolo ladani

 45. He is Wright anthu timakwiya ndi chilungamo that is why we can’t improve we have good. Players in Malawi but the system we use is not good . Start with the grounds we use very bad nanji Ku nursery kwathu Ku lower league gati po dyera n’gombe

 46. Sakunama mpira waku malawi supasana njala ndimadabwa anyamata ochuka kumwetsa zigoli mu supa ligi amalephera ku national team how mitengo imawapusitsa kwambiri mpira wakuno mitera mmmm ayi zanyanya

 47. Then he must resign and go, Analiko anzake achina Kim omwe anapanga zotheka ndi anyamata ake omwewo, osachulusa kunyoza

 48. Ndiye Apanga Bwanji Kuti Flames Iyambe Kuchita Bwino?Komanso Mmene Waonera Ma Team Mu Super League Athandizana Bwanji Ndi Ma Coach Akuno Kwathu?

 49. Its your task to change the way Flames is playing and that is why we are paying you ….. In addition to that, failing to lift the Flames up into Cosafa you’ll be sent back to Belgum and we’ll take back Kinah and Edie. Get note of that.

 50. Koma akunena zoona monga mmene kunali surestream muja inkamenya bwino barca barca nice football koma kulowa mu league kungowaponda ati mpira akenyela kwawo its more physical than creativity

 51. Kochi ndiwabwino koma ma plays anthu amadalila ufiti. Tsono akakumana ndi osatamba zimativuta tizingo sewela supa ligi basi. Fiti zokhozokha.

 52. True but we are waiting for him to show us the great thingis, may be our neirbours will stop roughing at us

 53. SAKUNAMA KOCHIYU, ine ndinazolowera kuonela English premier league, nde ndikamaonera za kumalawi izi zaphuphuphu aaaaa sizikoma ataaa. Mpira wa umozi umozi satimautha a Malawi kunena Chilungamo.

 54. ameneyu ndiye fodya akuyankhulayu! imyeyu tinamulemba ntchito kuti atithandize kulephera kwathu ndiye basi akonze osati adziyankhula za chingambwe zakezo.ngati zakoza adzipita kwawo coz adzingowononga ndalama zathu zamisonkho.

  • man wat u r saying is a non starter………even my Europe ma national team coach their job is to apply tactics according ndi opponent kukumana naye……zambiri ma player amakhala amakuziwa from their club’s……..wat u r saying it means iyeyo azikochatu team ili yose ya super league? to be honest pa Malawi pano soccer zero

  • @ Norman, tell them. Even pa company ntchito ya Chief Executive sikuphunzitsa anthu ntchito. Talent or skill ndi zachibadwa. Pali anthu omwe ali mmidzi omwe ali ndi skill than omwe akumenya ma clubs. Koma, exposure alibe. eg Mabvuto Lungu amkamenya ku mudzi, Mr. Gondwe ndikukamutenga kuti a bullets amuyese ndie munamuona bwanji?

  • Tinazolowera kunamizidwa that’s why tikuwona ngati chilungamochi ndi mbwerera …. Am a soccer fanatic koma it’s now a decade super league sindionera …. Soccer is in rural areas as Wellington Nowa has said ….

  • kodi akutsutsa ndi ndani?zomwe mzungu wakuyankhula ndi zoona ndiye imyeyo akoze zofowokazo. ndakudziwani enanu ndinu akampopi fc timu yanu ikungomenyetsa manja pamwala thats why mzungu wayankhula mawu amenewa coz adaona momwe achina sulumba,mulozi, sayilesi,chimango,anong’a,mkwate kumangopanga pakala pakala okha okha pagolo osapawona. tithokoze mzungu potiyankhulira

  • kodi Iyeyo akonza bwanji zofooka. ma coach a super league akuyenera kukonza hence atabwera ananena kuti he will work with super league coaches kuti the way of play in the league should match his tactics so its all up to super league coaches

 55. Ndimangodabwa, Eh! Ine ndi wamaule, eh! ine ndi wamanoma! AA! Mpira ngati wakung’ombe! That’s why I don’t support any team in Malawi. Suprisingly, some people still think the coach can play soccer. HA!

 56. ngat ukunena zoona ndeno iyeyo amafuna apeze zakupya kale nde amadzatan asanikwiitse wadyakale zambili!amalawiso tili ndisanje 2much rvg kumufewetsa mpamene mmalawi osamupatsa ndinjinga yomwe!!kupya ndimafupa omwe kulupodi

 57. NDADO MUKUNENA NDINU A NYUZI IYE AMADZiwa word yoti ndado.mukuzisisa nokha simunganene direct zomwe wanena iye mayazi koma muonjezere shot.kwanu ndikuti

 58. I know how hard is to swallow the truth,well said new coach,kukhala big fan wa flames mkulimba mtima wawa,moti ine sinkhumbira yayi dhala kuopa ngazikhweze!

  • maganizo opusa ngt RVG taona maplayer ife akumakanika kuchinya afta some tym mkukhala maplayer odalilika pochinya zigoli.

   couch do play a big role in players.zili ngt sukulu zimene zija akulu if th teach z gud its more likely kt ana atha kuchita bwino.

   sizamatabwa zakozo apa wangofuna kundiuza zomwe umapanga.awaphuzitse mpira!

 59. Translation ya chizungu sititenga each word kwa odabwa ndado….sindkudabwa ndzmene wanenazo poti ayiniake we oredy knw mpra wathu nd phalad compared nd pa zambia pompa wat am interested in ndzmene ngat wayankhula kut tithetsa bwnj u phala wathu if nt then azpta

  • Zoona otherwise ine zomwe ndawerenga from The Nation newspaper RVG wati watching the way some players were showing skills in the Superleague was like watching “tennis” ndiye poti chichewa nchathu a Malawi tennis atha kukhala “ndado, mbwelera, phuphuphu, etc”

%d bloggers like this: