A FAM mumakondela azungu – atelo a Malawi

RvG

‘Akakhala wakuda khungu ngati inu nomwe ndiye mumamuponya ku chipwete, akakhala mzungu koma si phuma lake.’

RvG
FAM ikukondera Mzungu

Uwu ndi uthenga umene a Malawi auza bungwe loona za mpira wa miyendo mu dziko lino la FAM pamene dzulo linalengeza kuti kampani ya ma lamya ya TNM yapeleka selula kwa mphunzitsi wa masewero a mpira wa miyendo, a Ron Van Geneugden (RVG).

A bungwe la FAM analemba pa tsamba lawo la pa Facebook kuti kampani ya lamyayi yapeleka selula ya ndalama za pafupifupi theka la miliyoni (K450,000) kwa RVG.

Pamwamba pa selula imeneyi imene ili yapamwamba kwambiri, ati bamboo RVG aziloledwa kuyimba phone kapena kutumiza uthenga mwaulere nthawi ina iliyonse ndinso mwayi opunguza makina a Intaneti umo afunile pa zaka ziwiri akhale ali m’dziko muno ngati mphunzitsi wa anyamata a Flames.

Izi zikuoneka kuti sizinakondweletse a Malawi ochuluka amene anakalemba pa tsamba la FAM pothilila man’gombe pa nkhaniyi.

“Kwa ma Kochi a ku Malawi ndiye simuwapatsa kanthu. Olo simu kadi yeniyeniyi. Zoduka mutu basi,” analemba choncho bamboo Harvey Kamanga.

“Ndi chifukwa chani izi sizimachitidwa kwa Bambo Kinnah Phiri kapena a Mtawali?” anadabwa bamboo John Cody.

“Achina Kinnah zimenezo sizinawachitikile bwanji? Mzungu ndi mzungu. Wakuda ndi wakuda. Tizingosaukilabeee (akudafe),” anatelo a Kul Wavisanga Khudzah.

“Mpira ku Malawi ndiye suzatukukanso. Taonani tikuyambitsa tokha kutsalana. Ife tizingokwapulidwa basi,” analemba choncho a Andrew Chiustis.

“Mayi Kalanga! Zonsezo chifukwa ndi mzungu?” anadabwa a Bisani Malinga.

Ena pongofuna kuonetsa mwano, anapempha FAM kuti mkuluyu amupatse mahule. Ati azikapumilapo.

Advertisement

102 Comments

 1. mo over mzunguyuso sadaphunzitseko national team yathuyi coz ma players adali atatengedwa kale ndi achina phiri kma busy ma fon galimoto akt dstv kogonaso ku hotel amalawi kuwopa mzungu

 2. Akuluakulu, kodi awa akumasowetsa anthuwa sangangomusowetsako winawake ku FAM chifukwatu ka ulamuliro aka ka FAM nde katimvetsa enafe kunuuuuuuuuunkha zedi…

 3. Kodi ameneyu ndi mzungu? Kkkkkk si m’bangaladesh wa ku Pakistan uyu muziwasinitsatu athuwa enawa ndi aphawi m’makwawomo athawa khondo uko kungofikira ubwana kuno, Nonsense

 4. Kkkkk iiii koma anthu akudafe sizinthu ndithu tapitan kwawo mukawone mmene amatisalila MA black fe.inu ndiye kumunjenjemela ngat ndi mulungu.

 5. Yes
  How can they give out all those ( Car, HD explorer Decoder, and Galaxy S7) ?
  Ever since no local coach has benefited from that.

 6. Vuto Ndilakuti Ku Fam Ophunzira Ndi Gome Basi Pakuti Mnzunguyu Izo Ndi Zomwe Ananena Mu Contract Ija Ndiye Walter Imamuvuta Kutanthauzira Ndiye Basi Akungoti Yes Bwana Apa Zangoyambika Koma Atikamadi Zenizeni Sinanga Aliyense Akungoti Dyo

 7. KKKKKKKKKKKKKK choti mudziwe nonse ndichoti mzungu amatengedwa superior than munthu wakuda, ndi m’mene ziliri chonchi mufune musafune. For example inuyo amend mukukambanu mungoganiza kuti pa nyumba panu pabwera mzungu mungata! Mmesa munjenjemera. Ka dziko kosauka ngati kano chilichonse chopempha kwa azungu. Tizasiya kunjenjemera azungu tikazakha anthu oziyimila patokha, koma pakali piano tiyiwale zimenezo.

 8. kupepera kugona kupusa uchitsilu kudontha kuchucha kugunata kumbwambwana mamina aanthu zidebe zobooka.kumupatsa zinthu zosezo zachan.kulipira chosavina.muzachenjer liti akanganya inu

 9. Penapake Amalawi Sitikondana Timadzidelera Kapena Kuti Kudelelana Chifukwa Nachi Mzungu Uyu Wangobwera Koma Zimene Mwamuchitira Anakakhala Mmalawi Sizikanatheka.Koma Taonani Posachedwapa Amanena Kuti Kuno Kumalawi Ma Players Aluso Alipo Atawonelera Game Ya NBB Ndi KB Mu Chifundo Charity Shield Panopa Tsopano Akuti Kumalawi Kulibe Mpira.Ndiye Bwanji Amathamanga Kulankhula Asanaonetsetse Apa Tangoyamba Kumene Kusewera TNM Koma Walankhula Kale Ndikuganiza Kuti Ntchito Imuvuta Ameneyu Alibe Masomphenya.Inde Mwamupatsa Zofunikira Zonse Simunalakwitse Ndiye Ma Coach Athu Akumalawinso Apatseninso Zofunikira Ngati Zimene Mwapatsira Mzunguyo Kuti Azigwilanso Ntchito Mosangalala.Tiyeni Tizikondana Amalawi.

 10. yes that’s true. we are respecting the outsiders by betraying our fellow Malawians. it would have been better if also the vice coash could be given the same things like RVG has.

 11. yes that’s true. we are respecting the outsiders by betraying our fellow Malawians. it would have been better if also the vice coash could be given the same things like RVG has.

 12. That thing is in the blood of a black man,we are racist against our own fellow brothers. We always treat a white person in a different way, This guy we busy spoiling will never deliver, those 2 games we lost against Mauritius, if it was kinna, chack and Young Chimodzi combined there was no way we could lose to such a team, Malawi needs Rvg but not as a head coach, we need him to partner with Water Nyamilandu in the offices to help football management.

 13. ya tru vuto ndlot akuiwala maplayer eni zn2 akusamala coach bas..Adakaikaso njira zna zot maplayer a Flames azinjoyako ena azislila kusewerako mu Flames ndy kut padakamakhala mpiksano wolimbrana malo mu team imenei..Flames players must also benifit more

 14. Amalawi kumvetsa chisoni,ngakhale kuwatumiza kunja kwa dziko,kuona waphikira makamaka akhala woera nkhungu amuti bwana.Mmalawi sadzamva

 15. not kukondela azungu. me am thinking that azungu aja they know what to do .and what the othet side can do kuti apushe ngini…..kunoko our coachez are too fast akangova zatchito kupupuluma safuna kutsatila ndondomeko … pamene azungu amayesesa kuyendetsa uso lawo ngat business pamene ife uphawi sitiganiza we rush just because national team……even our players amangosayina ma contract without understanding zomwe zili mkatimo… Ronny anabwela ndi agent kuno and they make a meeting ndi a fam night they agreed welfare yake and what he needs to do the good job if theyfail to do that what do you think

 16. Ndipo mmene nduuzionera zinthu ku fam-ku zuuonetsa mzunguyu makosanawa amvana naye heavy moti adziti lero kuumbudza mkazi wa #gunda mawa anyenga wa #Walter linalo kuthira batile wa #suleman kuchoka apo alinayenaye wa #gome kumalizira wa #casper

 17. Ndipo mmene nduuzionera zinthu ku fam-ku zuuonetsa mzunguyu makosanawa amvana naye heavy moti adziti lero kuumbudza mkazi wa #gunda mawa anyenga wa #Walter linalo kuthira batile wa #suleman kuchoka apo alinayenaye wa #gome kumalizira wa #casper

 18. poor management from FAM ending result also poor too. FAM too much greedy, right now you’re wasting a lot of money to buy expensive car yet you have very poor source of get money,FAM shame on you becoz of collecting taxes to poor people through the Govt.

 19. Zowonadi awonjeza ndithu w can estimate thats its more than 1000% kumunjenjemera mzungu mwina kuma coach achi less than 5% oh sorry & shit, partly to encourage kuti azititchura ngati zinyama kkkkkkkk

 20. Anakakhala Kuti Akuvutika Kochiyo, Bwezi Mukuwanena Afam Kut Amaziyambiranji?Koma Afam Akuyesesa Kupeza Masposa Mukuwanenaso Amalawi Munakhala Bwanji?Afam Akuyesesa Kut Kochiyo Asowe Ponamila

 21. This is most an fair isue,wat is problem of these guyz,they hav never given mwan coaches such gud things yet they xpectd coch 2 perfom gud resuit.h’eeeee so pathetic oh #God y!!!

 22. Apo ndye ndzoona ndpo flames singazawineso mizimu yanthu ambili ikudandaula ,,,,,ndalama zokubazija zimenezo zayamba kusefukila nyamilandu ndzako mwatasako kumeneko la 40 lizakwana mwandkwiisa hvy

 23. kunyumba kwanu mumatha kudyera masamba koma mlendo akabwera timazira tiwiri tokha mpakana mumukazingile NDE chimalawicho kaya or president akamabwera kwanuko muona msewu ukupalidwa kkkk

 24. nde kuMalawi kumeneko kufuna kupereka chithunzi chabwino kwa alendo , we have had so many Malawian coaches , who gave us good results e.g Kinnah but none of them was honoured as it is the case with RVG . Mpaka aziimba foni mwaulere kwa 2yrs? Above all , as an expatriate coach is being paid a lot of money. Hey!

 25. Paja mmalawi ndi mbava chilipo chimene akuzembera anthuwa gyz asamale nzungu ameneyo aberedwa ndithu otherwise akukonza kapasi .koma zoti angamatiwinise nzumgu ameneyo nde mmmm ndilibe chikhulupiro

 26. Kumvesa chisoni FAM!!! Kinnah munamupangilako chiani???? Great soccer hero!!!!! Mzungu kubwera pompo pompo den kuSunny side ya13million,car 22million,fone450000!!!! Mulungu akukhantheni mufe ndithu basi!!! Mzunguyo zonsezi azapita nazo inu mkukhala imviiiii mbuuuu kusowa pogwila!!!! Zitsimikizila mtundu waMalawi kuti team simuyikonda and sitikondana anthu akuda!!!

 27. Izi ndiye ndi Zoona ndiye Chonchi Ndikumati Team Ichita Bwino Nanga achina Kinnah amasowa ndi kabaza yemwe even phone masowa ndi zte yemwe but mzunguyi mpaka galimoto hahaha Ndalama zanga za msonkho izo

Comments are closed.