Osamavala za chi Malawi kuno: aphungu akana zovala za chi Malawi

Advertisement
Parliament

Phungu wa nyumba ya malamulo wa dera la pakati mu boma la Mwanza, a Davis Katsonga, aletsedwa kupita ku nyumba ya malamulo kamba kovala ka chisoti ka chikhalidwe chawo.

Davis Katsonga
Katsonga: Aimisidwa ku nyumba ya malamulo.

A Katsonga amene ndi Phungu wa chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) apitikitsidwa mu nyumba ya malamulo lachitatu ati kamba anaika nthini kumutu.

Wachiwiri kwa sipikala wa nyumba ya malamulo, a Clement Chiwaya anathamangitsa Bambo Katsonga ati chifukwa momwe anavalila sizogwilizana ndi ndondomeko ya nyumba ya malamulo.

“Dzulo tinakuletsani kuvala chonchi, lero mwabwelezanso. Nyamukani muzipita,” anatelo a Chiwaya.

Iwo alamula a Katsonga kuti asaoneke mu nyumba ya malamulo kwa masiku asanu ndi awiri kamba koti anavala ka chisoti kachingoni.

 

Advertisement

65 Comments

  1. Ndichifukwa chake timalankhulanso ENGLISH kunyumba yamalamulo m’malo molankhula CHICHEWA chathu akuti kufuna kusangalatsa AZUNGU.Pa MOZAMBIQUE pompa amakambirana MUCHIPWITIKIZI chawo kuti aliyense ADZIMVAAA.Popanga CAMPAIGN mumatilankhula CHICHEWA koma mukapita kumeneko kumakambirana mu ENGLISH.2019 mukamadzapanganso CAMPAIGN muzapangenso mu ENGLISH muwone ngati MUNGADZAVOTELEDWENSOOOOOOOOOOOOOOOOO

  2. Siwonse Wochita bwino amene ali ozindikira even ife anthu wamba timangovala zithu zina Ku malo osayenera , koma ngati tsiku limenero mumakambira za cultural there is no any problem

  3. Zinthuzina zimafunika dongosolo sizongodzuka basi lero ndivala pant yekha ku paliament ayi……..pamafunika kugwirizana kuti guyz mawa tikavale mapant okha ……

  4. Retrogressive! They need a learning visit to Nigerian Federal Assembly, be proud of ur culture. The best would have been to allocate days for cultural dressing

  5. Nonses azikzmbirana za development osati zachivalidwe just imagine is there any effect towards devlpmnt or akungofuna azingokangana ndizopanda pake mumalo molimbana ndi corruption ndi kutukula dziko

  6. Man U was 6th last year (2016)
    Man U are 6th this year (2017)
    Man U were 6th 3 months ago
    Man U were 6th 2 months ago
    Man U were 6th 1 month ago
    Man U are still 6th this month
    Man U are still 6th this week
    Man U are still 6th yesterday
    Man U are still 6th today
    Man U are still 6th right now

  7. Malawi 24 stupit kagulu akakalindi dziazitolankhani dzitsilu Zokhazokha nkhani yakatsonga siilichonchi sananekuti osavala zachimalawi bt malamulo akuletsa phungu wachimna kuvala chinthu mmutu y mmafuna mzizondotsa anthu nditinkhani tanu taumve,,

  8. Munthu wavala buluku la mzungu, jekete la mzungu, thayo ya mzungu, nsapato ya mzungu, lamba wa mzungu, mphete ya mzungu, mandala a mzungu, panti wa mzungu, kumayankhula chinenero cha mzungu, koma kungovala ka mthini kosonyeza chikhalidwe chake likhale tchimo?

    1. Hamba = yenda
      Yedwa= yekha

      nquma
      .decide, determined (among other meanings)

      nqumayo

      he that is determined/ has decided

      Therefore, Hambayedwa Nqumayo in this context should mean he who has decided to walk alone.

  9. owo auzeni kuti ifenso takana za kunja makamaka za amuna kapena akazi okhaokha kukwatirana…mmalo mokambirana chothetsa/kuchepetsa uphawi komanso mavuto amene akulepheretsa chitukulo osati chifukwa cha mavalidwe. sipresident anati buy malawian…. umbuli otheratu umeneu iyaaaa

  10. We need to re-visit the ideas of one of the greatest and best African President , the Upright Man ” Thomas Sankara”. He believed in African way not Western way. Its higher time we start believing in our own culture including African dressing code in order to promote our own culture thereby uplifting our economy.

  11. Bwana Katsonga mutisokonezela zinthu kumalawi kuno.Nankha Chakwela naye akazalowa mnyumbayo atabvala makanja wake ndiye kuti akulakwa ?

  12. Malawi kuli mbunzi zokhazokha basi walakwa munthu kuvala mwachikhalidwe cha kwawo shame!

Comments are closed.