Neba wamenyedwanso ku Lilongwe

115

Silver Strikers yasosola Bullets.

Ikakuona litsiro sikata.

Patatha masiku chabe ataona mbonaona kumpoto, Neba wakumananso ndi mazangazime mu mzinda wa Lilongwe pamene wapamanthidwa ndi a Silver Strikers.

Pa masewelo amene anachitikila pa bwalo la za masewelo la Bingu National, timu ya Silver inaonetsetsa kuti Maule apitilize kumwa wa mandimu.

Chigoli cha Victor Limbani chomwe chinabwela patangotsala mphindi zinayi kuti mpira uthe ndicho chinadzetsa misonzi ku banja la ma palestina.

Mu nyengo ino ya mpira, Maule aluza kachiwili kotsatizana.

 

Share.
  • Opinion