Nyerere, RVG akukupatsani theng’eneng’ene

82

Pamene masewera a chikho cha ma timu asanu ndi atatu mu chikho cha Airtel chomwe chifumbire kuyambira lowelukali, anthu ena otsata za masewera a mpira wa miyendo ati chikhochi chikhalangati ngati kukumba madzi pa thathwe kuchipambana kuti wina akachimwelere.

Ambiri akuti kubwera kwa m’phunzitsi wa timu yayikulu ya dziko lino Ronny Van Geneugden (RVG) kupereka mpishupishu kwambiri kwa ma timu omwe amachalira kuti mwina ayenda moyera potengera mbiri zawo.

Ronny Van Geneugden

Geneugden wayambapo kusaka osewera.

Malingama ndi yemwe adali technical director wa timu ya Nyasa Big Bullets Billy Tewesa, iye wanenetsa kuti za ulendo uno zikhala za mlingo wina chifukwa osewera aliyense afuna kuti awonedwe ndi RVG mcholinga chofuna kudzigulira malo mu timu yayikulu ya dziko.

M’mawu awo a Tewesa ati Airtel top 8 ipereka mwayi kwambiri kwa osewerawa chifukwa ukhala mpikisano wa ma timu owerengeka chabe kusiyana ndi chikho chachikulu mdziko muno cha TNM super league chomwe chimaitana ma timu 16.

“Anyamata alimbikira kwambiri nthawi imeneyi kuti m’phunzitsi ndi omuthandizira ake awawone kotero kamba ka zimenezi ukhala mpira wa dzaoneni munditsimikiza ndipo kutenga chikho chenechi sukhala mtunda wa masewera” adatero Tewesa poyankhula ndi wailesi ina mdziko muno.

Koma malingana ndi wamkulu wa timu ya Wanderers Steve Madeira, iwo atj ali ndi chitsimikizo chonse kuti chikho cha Airtel chomwe changokhazikitsidwa kumene chaka chino atenganso kumka nacho ku nsewu wa Lali Lubani monga mwa mbiri yawo. Pamene iye wanena kuti 15 million ndi ndalama zomwe iwo ali nazo nkhuli kwambiri.

Madeira wanenetsa kuti Manoma akomzeka kwambiri kuti ateteze mbiri yawo yotenga chikho chilichonse chomwe mchoyamba m’maso mwa a Malawi ku nkhani zododa chikopa.

Koma m’mawu ake sabata zapitazo RVG adati iye ngati m’phuzitsi adzisankha osewera malingana ndi umo m’mene akukankhira chikopa pa bwalo, osati mbiri ya munthu kuti wakhala akusewera kwa zaka zochuluka mu timu ya dzikoyi. Izi zatsimikizadi kuti masewera a chaka chino afumbiradi zomwe sizikhala zophwekwa kwa akatswiri omwe akhala akunyamula dzikho monga cha Standard Bank, Carlsberg, Presidential, FISD.

Chikho cha mu Airtel top 8 chiyamba ndi ma timu a Silver Strikers kuphana ndi Bullets pa Bingu national stadium, pamene MAFCO idzalandile asilikali amzawo a Moyale pa bwalo la Chitowe ku Nkhotakota.

Sizidathere pompa koma lamulungu lake Beforward Wanderers idzaphana ndi timu yomwe iwo amatapako mphamvu zawo nthawi zambiri ya Azam Tigers pa bwalo la Balaka ndipo akatswiri a chikho cha 2016 super league Kamuzu Barracks asulana msulizo ndi Blue eagles pa Civo.

Share.
  • Opinion