Malawi 24

Zavuta kumpanda, chinsalu chija chang’ambika: Bushiri ati ndi wa chimasomaso

Likanakhala sewerotu tikanati mutu wake ndi _Ndani ankadziwa_. Koma ili si sewerotu, iyi ndi ndeu yeniyeni yong’ambilana ma khamusolo pa msika.

Amene anali mneneri wa mneneri a Shepherd Bushiri, Bambo Kelvin Sulugwe, ayamba kuvumbulutsa zina mwa zinsinsi za mbuye wawo wakaleyu.

Nthawi imeneyo alibe nkhawa

A Sulugwe amene anakhalapo akuthila ukali aliyense okaika kuti Bushiri ndi mtumiki wa Ambuye ayamba kunena nkhani za ku chipinda kwa a Bushiri pa tsamba lawo la pa Facebook.

“Ine sikuti ndimafuna kunena zoyipa za a Bushiri iyayi, koma anthu a kwa Bushiri akuchita kundiputa. Ndipo ndatopa ndi kunyozedwa. Tsopano ndithila moto,” anatelo Bambo Sulugwe pofuna kulongosola mbali yawo.

Bambo Sulugwe ati ndi okhumudwa kuti Mneneri Bushiri ndi anthu ake akufuna kuwaonetsa ngati iwo ndiwo adali kavuwevuwe owadanitsa a Bushiri ndi atsogoleri a dziko.

“Akulemba ngati kuti ine ndiye ndimawatsogolera a Bushiri kuchitila chipongwe atsogoleri. Zimenezi sindikugwilizana nazo. Asandiyipitsile mbiri,” anatelo a Sulugwe

 

Ya ine inali ntchito

Sulugwe: Inali ntchito

Bambo Sulugwe ati zonse zimene iwo amalemba zinali zotumidwa ndi a Bushiri chifukwa iwo anali ogwila ntchito chabe.

Iwo ananena izi pa chiwelu pofuna kuthilila ndemanga pa nkhani yoti a Bushiri ayamba kukamba za nzeru pamene alemba ntchito Bambo Ephraim Nyondo kuti akhale mneneri wawo.

Tsamba lina linalemba kuti a Bushiri atalemba ntchito a Nyondo amene ndi ophunzila kuposa a Sulugwe, ati a Bushiri ayamba kulongosoka.

Ndipo Bushiri ndi wa chimasomaso, akubelekela ana amayi omutsatila

A Sulugwe aululanso kuti Bambo Bushiri ndi Mkulu okonda zovulavula izi ndipo abelekelapo ana amayi ndi asungwana owatsatila.

Iwo anaulula izi pamene amathila ukali mkulu wina wa kwa Bushiri, Bambo Thocco Phiri.

‘Bushiri ndi wachimasomaso’, akutero

“Inu a Thocco Phiri, khalani chete. Inu mukanazifunsa kaye kuti ndi chifukwa chani anakukakamizani kukwatila mkazi wanu wamkuluyo,” a Sulugwe analemba kusonyeza kuti kalipokalipo pa ukwati wa a Phiri.

A Sulugwe kenako anaulula chimene chinachitika.

“Tamuona mwana wakoyo, safanana ndi iwe. Amafanana ndi Kudzodza,” anazimbayitsa kunena a Bushiri kuti ndikudzodza.

A Sulugwe anapitiliza kuulula kuti ana amene Bambo Bushiri amabeleka ndi akazi okhaokha. Mu kufotokoza kwawo, zikukhala ngati a Bushiri ndi kakhalidwe kawo komwaza tiana tatikazi.

Ululani zambiri a Sulugwe

A Malawi amene akondwa ndi nkhani zimene a Sulugwe akuulula apempha mkuluyi kuti apitilize kuulula zambiri zokhudza mtumiki Bushiri.

“Pitilizani ndithu, tikudikila timvenso za matsenga ndi zozizwa zomwe Bambo Bushiri amachita,” akutelo a Malawi ena.