Zativutanso!
A Malawi ali pakalikiliki kuthamangila ku ma okala kuti apeze nawo mwayi ogula shuga yemwe akusowa zedi mdziko muno.
Shuga wasala ochepa zedi mu magolosale aakulu ngati Shoprite, Peoples, Sana Cash and Carry komanso Chipiku.

Malingana ndi maripoti, izi zili chomwechi chotele kamba koti kuli mpungwepungwe pa nkhani za mgwilizano wa pakati pa kompani yomwe imapanga shugayu ya Illovo komanso makampani onyamula shuga kuchokera kumafikitale kupitisa mmisika. Koma a Illovo sanayankhulebe kalikonse pa za nkhaniyi.
Mu Shoprite mwachitsanzo munthu sakuloredwa kugula mapaketi opitilira asanu ndi limodzi (5) . Izi zaikidwa kuti aliyense aguleko shugayu yemwe akugulidwa ndi anthu mokanganiliana.
Izinso zapangisa kuti shuga afike pa mitengo ya K950 komanso K1000 kupyole mtengo ovomelezeka wa K750.
Mmene zililimu, pofika sabata la mmawa, shuga akhala atatheratu kamba koti mumagolosale ambiri watheratu.
Pakali pano bungwe lowona ufulu wa ogula la Consumers Association of Malawi (CAMA) lati kampani ya Illovo iyenera kunena ku mtundu wa a Malawi vuto leni leni la kusowa kwa shugayu.
IIllovo ndi kompani yokhayo yomwe imapanga shuga ku Malawi.
Latest vacancies
242 thoughts on “Pavuta pa msika: Shuga wasowa”
Comments are closed.











Kodi shuga amene timapangayu akupita kuti gayesi osabisatu shuga
Write a comment…
shaaa dziko mpaka lomasowa shuga mavuto sazatha basii
that y ndimangoipota
Anthu nonse omwe mukunyoza boma nkhani yasugar mitu yonu sigwila ayi. Sichinthu chachilendo sugar kusowa kumalawi
asanu ndi limodzi(5) kkkkkkkkkkkkkkkkkkkkk
Aaa ndizingomwa juice wa Wakawaka k30 chikapu ndeeeee
Kkkkk, asanu ndi limodzi nkudzati (5)? Scribes! Hey!
Ife tikumagula wa ku mozambique pa lizulu @ k800
Apa guyz tea xitimwaxo mpak grand mmmmm km malawi waonongek bc
its time to learn how to leave without sugar, we can copy from China people.
Anthu enanu muli m’mabvuto akulu ganyu wabvuta. Kodi panyumba kapena ndinene kuti pabanja zinthu zogwilitsa ntchito monga mchere,sopo,macheso,suga ndi zina zikatha amauza mwana kuti akapeze zinthuzo?Mwina kwinako zimatero,koma kwathu kuno timauza amene ali oyang’anira pabanjapo kuti athe kutithandiza.Ndiye ena mukuti tisaloze chala boma kapena pulezidenti ndiye chabwino tasintha inuyo inu tipatseni kapena tulutsani suga anthu asabvutike nkulimbirana pogula.Paja zinthu zikavuta olamula amakhalanso otsutsa muja idachitira UDF atachoka Bingu nkuyamba chake chipani ndiponso DPP idalinso yotsutsa nthawi ijayi atakhala pa mpando mayi Joice Banda pomwe dppyo ndiye inkalamula boma.Zinthu zabvuta kumpanda madzi achita katondo.
mwina ayibaso Sugar kumeneko, nanga wasowa bwanji.
Ndiwo Ana A Munthalika Ulamuliro Tidauzolowera Sizachilendo(chimanga Chochuluka,ndalama Kusowa,malipiro Kuchedwa,ngongole Zambiri Ndi Kusowa Kwamafuta Omwe Asowaso Posachedwa)komabe Timakunyadirani Poti Ntidziwitsa Kuti Sukulu Sichotsa Uchitsiru Moti Ulemu Wanu
https://www.facebook.com/LCPMWOFFICIAL/?ref=your_pages
zintchito za diphiphi ndi kunda palibepo zachilendo apa!
Kkkkkkk mizimbe yatha ku farm
Let me eat zimbe Ku NCHALO kuno…mundipeza Ku KALULU or Ku area 4
It started like this with the late Big Kahuna nd now this young Kahuna is following the footsteps of the bro
Ife ndi abawa inu makape omwa sugar munya nayo pamodzi ndi uyo wakhala pampando