A Kamlepo kukhala ngati alowa m’tchire muja: sakudziwika komwe ali


Kamlepo Kalua

Bambo Kamlepo Kalua amene anamenyela ufulu wa zipani zambiri, ati asowa.

Bambo Kalua amene ndi Phungu mu dera la Kummawa mu boma la Rumphi ati sakudziwika kumene ali. Wanena izi ndi mwana wawo, Penjani.

Malingana ndi Penjani, amene amazitcha kuti Fredokiss pa nkhani zoyimba, Bambo ake asowa pa nthawi imene akufufuzidwa ndi a Polisi komanso bungwe la misonkho.

Kamlepo Kalua
A Kamlepo Kalua sakuziwika komwe ali.

A Kalua akuganizilidwa kuti analowetsa galimoto mu dziko muno mozemba msonkho.

Koma anthu ena akuti boma la a Peter Mutharika likungofuna kuzunza a Kalua chifukwa akhala akulidzudzula mopanda mantha.

“Ife monga a ku banja zikutiopsa, Bambo wathu sachoka osalawila ngati umu zachitikilamu,” adatelo Penjani.

Iye anaonjezelapo kuti nthawi imene atate ake asowelayi ndi yopatsa nkhawa malinga ndi kuti anali akuthupsa boma.

Koma anthu ena aseka mwachikhakhali nkhani yoti a Kalua asowa.

“Walowa m’tchire ameneyo, paja anaopsezapo kutelo,” walemba mkulu wina pa Facebook.

Mmbuyomu a Kalua ankaopseza mtsogoleri wakale wa dziko lino, a Bakili Muluzi, kuti iwo azalowa m’tchire posakondwa ndi utsogoleri wa a Muluzi.

Latest vacancies

199 thoughts on “A Kamlepo kukhala ngati alowa m’tchire muja: sakudziwika komwe ali”

    1. dats depromatic… even if he can go to india he cn do what ever he wonts, worlds political rule dat was issued in 1859

  1. Koma tisapenze tafa ndiye kuti iwe nala ulipamabvuto ngati njoka palibe chimene walakwa ndiue ukusowensa anthinmunjira imen e ikufuna

Comments are closed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading