Achinyamata ojambulitsila kumanda agwidwa ufiti

Advertisement

Kufuna kuonedwa ndi kukondedwa ndi aliyense pa masamba a mchezo ndi khumbo la wa chinyamata aliyense pa dziko malinga ndi zifukwa zake koma ku Malawi zafika pa mlingo wachilendo pamene achinyamata ayamba kulowa mpaka m’manda.

Izi zavundukuka pamene achinyamata ena ku Blantyre ajambulitsa zithunzi zawo ku malo kogona anthu omwe ndi omwalira ncholinga chofuna kutchuka ndi kuonedwa ndi anthu ambiri kuti iwo ndi a m’dziwi ndinso ozitsata.

Achinyamata awa anagundika kutenga zithunzi kumanda.

Zithunzizi zomwe zikuyenda pa masamba a mchezo ambiri zadzetsa nthumazi kwa amalawi ambiri ponena kuti izi nzachilendo komanso nzolaula mudzi.

Malingana ndi maso akuthwa a Malawi24, anthu ochuluka poyikira ndemanga zithunzizi akuti ka khalidwe ka chilendoka nkosowa ulemu komanso kupandiratu khalidwe ndinso kuperewera nzeru ndi umunthu.

M’modzi mwa oyimba yemwe adapambana mpikisano wa oyimba a chamba cha Hip-hop Martse pothilira ndemanga yake wati izi nza uchitsiru weni-weni opanda nawo mzeru.

“Zoti ndife asangalatsi nzodziwika komabe tikuyenera kusungabe chikhalidwe chathu ngati amalawi pali njira zambiri zotchukira koma zinazi mudzangonong’oneza nazo bondo ndithu kaya mwamva anthu otsetseretsa ma thalauza inu kaya ndi uyooh,” adawasakatula Martse.

Maganizo a mwini miyanda-miyanda kuti zithunzi zonga izi ndi pongofuna kudziwika chabe, pamene iwo akuti achinyamatawa kujambulitsira kumanda zidali zokonza.

Pa masamba ambiri a mchezo achinyamata ambiri achitauni amapikisana zithunzi ncholinga chofuna kupeza chidwi kuchokera kwa anthu ochuluka, mwakuti malo amene munthu wajambulitsa ndi amene amapereka chidwi kwambiri kuposa iye munthuyo.

Advertisement

2 Comments

Comments are closed.