A PP ndiwo adachotsa a Chilima pa udindo

5

Boma la Malawi lati likudziwa kuti anthu otsatila Mayi Joyce Banda ndiwo adalemba kalata yoti a Saulos Chilima atula pansi udindo.

Malinga ndi mneneri wa boma, a Nicolas Dausi, amene analinso mkulu wa u kazitape mu dziko lino, a boma ti akudziwa anthu amene adachita mtopola onama bodza kuti a Chilima anyanyala udindo wa wachiwili kwa mtsogoleri wa dziko lino.

A Dausi alavulira chipani cha PP moto.

“Mwanaaa, anthu ake tikuwadziwa adachita upandu umenewu,” adatero a Dausi pothilila ndemanga pa nkhaniyi.

“Ndipo anthu ake sikuti angabisale ayi,” adaonjezela chotelo. “Anthu amenewa ndi amene anathawa atangoluza zisankho zija, pano ayamba kufuna kudzetsa mpungwepungwe pakati pathu.”

Ngakhale a Dausi anakana kutchula dzina la anthuwa, anthu akuganiza kuti iwo amanena anthu a chipani chotsitsa cha Peoples’ (PP).

“Pakali pano sitikutchula mayina koma anthu amenewa ndithu anjatidwa ndi a Polisi ngakhale abisale motani,” anaopseza a Dausi.

Mtsogoleri wakale wa dziko lino a Mayi Joyce Banda anabanduka atangogonja pa zisankho za 2014 ndipo iwo akhala akudumphadumpha ku mayiko a kunja.

A Dausi potchula kuti anthu adalemba kalatawo ndi otsatira Mayi Banda zapangitsa anthu kuona ngati akunena anthu a PP.

Share.

5 Comments

Leave a Reply