Palibe kuvota pompano, tidikile kaye Bajeti

Advertisement

Bungwe loyendetsa zisankho m’dziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) latsindika kuti zisankho za pa dera zomwe zimayembekezeka kuchitika m’ma dera ena a dziko lino zidikira ndondomeko ya za chuma ya boma.

Malingana ndi wapampando wa bungwe la MEC Jane Ansah, ntchito yokonzekera zisankhoyi itenga nthawi chifukwa boma lapereka ndalama zosakwanira ku bungweli kuti limalize ndondomeko zonse za chisankho.

Jane Ansah
Justice Jane Ansah: Boma lilibe ndalama.

Polankhula kwa anthu a dera la Lilongwe City South East lachitatu a Ansah anati iwo adikira ndalama zonse kuchokera ku boma mu ndondomeko ya za chuma yomwe ikubwera, koma iwo anati ndalama zomwe analandira kale azigwiritsa ntchito zina zokonzekera chisankho cha paderachi monga kulemba ndi kuphunzitsa anthu ozagwira ntchito ya kalembera.

“Ndi zofunika kuti ndikudziwitseni kuti yokonzekerayi itengako nthawi kamba koti kuti boma (treasury) lilibe ndalama zoti tipange chisankho malingana ndi ndondomeko yathu yomwe tinakonza kuti tichite chisankho pa 06 June 2017” anatero Jane Ansah.

Wapampandoyu anatsindika kuti boma lakanika kupereka ndalama zokwanira chifukwa cha mavuto ogwa mwadzidzidzi omwe akuta dziko lino.

“Izi zachitika malingana ndi mavuto ogwa mwadzidzidzi amene dziko lino lakhala likukumana nawo monga ng’amba, kusefukira kwa madzi, njala ndi zina zotero kotero kuti tindalama timene tilipo boma ligwiritsa ntchito zina monga kugula mankhwala mu zipatala, ndi zina zofunika mwa nsanga,” anaonjezera choncho a Ansah.

Popereka thima lodekha kwa anthu a derali iwo anatsimikizira anthu a derali kuti iwo akudziwa kufunika kokhala ndi oyimira derali ndipo akuyesetsa kukambirana ndi boma kuti ndondomekozi ziyende mwa m’mangum’mangu

Bungweli limayenera kuchititsa chisankho cha padera ku dera la Lilongwe City South East pa 6 June chaka chino malingana ndi chigamulo cha bwalo la milandu la apilo (Supreme court of Appeal).

Malamulo a bungwe oyendetsa chisankho amati chisankho chapadera chimayenera kuchitika pasanadutse miyezi iwiri kuchokera pamene dera lakhala lopanda oliyimira.