Ogwila ku ADMARC achita u Chaponda

Advertisement
Admarc Malawi

Nkhani ya kuba kwa chimanga idakalibe m’bwalo ngakhale mkulu amene anali induna yoona za malimidwe a George Chaponda adachotsedwa.

Mkulu wina ogwila ntchito ku ADMARC mu boma la Nsanje, watsekeledwa ataponda matumba a chimanga okwana 107.

Matumbawa akuikidwa pa mtengo okwana K1.6 Miliyoni.

Malinga ndi a polisi a mu boma la Nsanje, iwo anjata a Matthias Muyatso a zaka 26 powaganizila kuti adachita za u Chaponda ndi matumba achimangawa.

Malinga ndi mneneri wa a Polisi mu boma la Nsanje, a Agness Zalakoma, Bambo Muyatso adapezeka ndi matumba 107 olemela 50Kg thumba lililonse pamene a Polisi adachita chipikisheni kwa ogwila ntchito pa ADMARC ya Tengani pofuna kulondola umo matumba a chimanga adayendela.

“Pa chipikisheni chathu, tinapeza kuti bamboo Muyatso anali kusunga matumba 107,” adatelo a Zalakoma.

A Muyatso agwidwa patangotha ma sabata ochepa mkulu wina ogwila pa ADMARC ya pa Nsanje atagwidwa naye ndi matumba a chimanga okuba.