Inu, ati musiye kutukwana pa Facebook

233

Saliokha a Peter.

Patangidutsa tsiku mtsogoleri wa dziko lino ataopseza kuti boma lake linjata anthu onse osamalika pa Facebook, naye sipikala wa nyumba ya malamulo walangiza a Malawi kuti pa Facebook sipotukwanila.

Richard Msowoya

Msowoya akudana ndi mmene a Malawi akugwilisila ntchito makina a intaneti.

Malingana ndi a Richard Msowoya amene ndi sipikala wa nyumba ya malamulo komanso wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani chotsutsa cha Kongeresi, pa Facebook simalo onyozelapo atsogoleri.

“Ndikulangizeni achinyamata, muleke kunyoza atsogoleri anu pa Facebook,” anatelo a Msowoya polankhula kwa ana amene asonkhana mu mzinda wa Lilongwe ku mkumano wa aphungu a ana.

“Achinyamata ambiri mukutha nthawi kukhala pa Facebook ndi kumatukwana atsogoleri anu, kodi zimenezo zipindula chani?” anafunsa a Msowoya.

Iwo anamema achinyamata kuti akuyenela kutengapo gawo potukula dziko lino.

“Palibe zomati ine ndachepa, aliyense akuyenela kutengapo gawo popititsa dziko lino patsogolo,” anatelo a Msowoya.

 

Share.
  • Opinion