Midoli, Win ikupangabe makani pamsika

0

Ngakhale bungwe loyeza zakudya m’dziko muno la Malawi Bureau of Standards (MBS) lidaletsa mowa wa mmabotolo a plastic, mowawu ukupezekabe pa msika mma boma ambiri mdziko muno.

Diso lakuthwa la Malawi24 lapeza kuti mowawu omwe ukukhalabe mu mabotolo a plastic ukugulitsidwa m’misika ngakhale MBS idaletsa zomwe zasonyeza kuti ogulitsa sakufuna kumvera zomwe MBS ikufuna.

Mkalabongo

Mowa onga uwu ulibe pa msika.

Ngakhale kupakila mowa mu ma pakete komanso m’mabotolo a plastic kuli koletsedwa M’malawi muno Malawi24 yapeza kut ku Lilongwe madera ena monga area 36, 23, Mtandile ndi Mitundu mowawu ukupezekabe pa Nsika.

Mu mzinda wa zamalonda mdziko muno wa Blantyre, Midoli, win, Shooter ndi mowa wina ukupezekabe mu ma dera ena monga Mbayani, Manje, Bangwe ndi ma dera ochuluka ena mu Mzindawu.

Malingana ndi Chigamulo kuchokera ku bwalo la milandu Mdziko muno pa 4 January lidaikira kumbuyo MBS kuti kupanga ndi kulongedza ndi kugulitsa mowa mma sacheti ndi m’mabotolo a plastic mkoletsedwaa.

Mchaka cha 2010 kuletsa mowa wa mtunduwu kudaomba m’golo pamene ma kampane opanga ndi kupakila mowawu adakatenga chiletso ku bwalo la milandu kutsutsana ndi kukanizidwa kupanga mowawu.

M’malingana ndi MBS, iwo anenetsa kuti ulendo uno palibe kampani yomwe ichite matukutuku kupangabe mowawu ndi kulongedza m’mabotolo a plastic.

“MBS ikudziwitsa anthu ndi ma kampani onse opanga mowa wa ma spirits kuti ulendo uno akwanilitsa kuletsa mowawu (MBS therefore wushes to inform the general public and manufacturees of the spiritious liquor that it will implement the ban following the rulling the general public and all manufacturers are heteby advised to comply with the MBS Act Cap 51:02 as stipulated in MS 210 (1990)”. idatero MBS mchikalat chawo.

Share.

Leave a Reply