Kafukufuku wa ntchetche akudwalitsa mutu a Mutharika

Advertisement
Peter Mutharika

…A Peter ndiye sakugona tulo

Patapita masiku angapo mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika atanyoza kafukufuku wina amene anapeza kuti iwo alibe chikoka, a Mutharika abwelezanso kulalatila akulu amene anapanga kafukufuku ameneyi.

Peter Mutharika
A Mutharika ndi okwiya zedi.

Polankhula kwa anthu amene anasonkhana kuwachingamila a Mutharika mu mzinda wa Lilongwe, a Mutharika ananena kuti iwo anakali ndi chikoka.

“Onani khwimbi lonse liri apali, zoona wina ndi kumati ine ndilibe chikoka?” analira mokweza a Mutharika.

Iwo ananyoza kafukufuku ameneyi masabata apitawo kuti anapangidwa pakati pa ntchetche ati chifukwa anapeza zinthu za bodza.

“Taonani anthu onsewa ali pano, ndiye wina azikati ndilibe chikoka, amafunsa ntchetche kapena chani?” adakalipa a Mutharika.

Koma chodabwitsa ndi choti a Mutharika tsopano atanganidwa kutsutsana ndi kafukufuku amene akuti adapangidwa pakati pa ntchetche.

Advertisement

3 Comments

  1. Tiyeni naye ameneyu nayenso watsala pang’ono kugwa. Akupanga zomwe ankapanga mkuluwake atatsala pang’ono kugwa. Asamanyoze a Malawi ngati kuti ndife anthu opusa. Kafukufuku akakhala okomera iyeyo salankhula kanthu. It’s not that things will go your way always.

Comments are closed.