Kachama sapepesa

1

Mkulu wa Malawi Police, bambo Lexten Kachama wamenyetsa nkhwangwa pamwala kuti iye, ngati yemwe anakhalapo pa udindowu a Peter Mukhitho, sapepesa kwa Jessie Kabwila.

A Kabwila, omwe ndi phungu wa chipani cha Kongelesi anamangidwa pamodzi ndi anzawo pamulandu ofuna kupandukira boma.

Lexten Kachama

Kachama: sindipepesa

Koma bwalo lalikulu loweruza milandu lati a police analakwitsa kuthira unyolo anthuwa. Khotili lalamula boma kuti lipereke dipo ndi chindapusa kwa a Kabwila.

Atafunsidwa a Kachama kuti iwo anachita phuma pomanga a Kabwila, iwo anayankhula motumbwa kuti sakuonapo kulakwika pakumanga anthuwa poti mulandu ofuna kugwetsa boma si ntchezero.

“Ife apolisi sitipepesa pogwira ntchito yathu. Mlandu oukira boma si tubvi ayi. Choncho palibe chifukwa chopepesera,” anatero a Kachama.

Share.

One Comment

  1. Inusotu kumaganiza, ndi udindotu uwu umatha, mukulankhula ngati anzanu sadya sima yomwe inu mudya bwanji?

    Umunewo sindiye ukulu pa udindo, mukupereka khalidwe lotani ku dziko? Osazichepesa ndikupepesa bwanji?
    Poti ndi osusa boma ndiye anyozeke ndi iweyo, no! Be matured mr. man

%d bloggers like this: