Hahaha mpaka Gerald Phiri, ndiye sewerotu – wanyogodola Peterkins Kayira

Advertisement
Gerald Phiri
Gerald Phiri
Phiri(Pakati) wasankhidwa kukhala mphunzitsi wa timu ya dziko lino.

A FAM ndi kutheka amayesa akonza zinthu koma apa ayi ndithu, iwo sanakondweletse katswiri otsatila mpira wa miyendo a Peterkins Kayira.

A Kayira ati ndi okhumudwa kuti bungwe loyang’anila za mpira wa miyendo mu dziko muno, FAM, lasankha Bambo Gerald Phiri kuti akhale mphunzitsi wa timu ya dziko lino.

“Iyi ndi ngozi ndithu, napolo wa ku Phalombe uyu,” anena monyogodola a Kayira.

“Sikuti ndikunyozetsa a Gerald Phiri ndi owathandizila awo, koma ndikuona kuti adya mfulumila potenga udindo umenewu,” a Kayira anaonjezelapo.

Iwo anati bungwe la FAM limayenela kuona lokha ngati a Phiri angathe kupikisana ndi anthu ena amene aphunzitsapo timu ya dziko lino.

“Inu mungafanizile Kinnah, Jack Chamangwana, Young Chimodzi ndi Yasin Osman kwa ana atengawa?” a Kayira anadabwa.

Advertisement