A Msonda ndi a Brian Banda avundulana pa wayilesi

Ken Msonda

Membala wa Democratic Progressive Party (DPP) a Ken Msonda avundulana ndi mtolankhani odziwika bwino m’dziko muno a Brian Banda.

A Msonda adasambwadzana ndi mtolankhani wa wailesi ya Times Brian Banda yemwe ndi mtolankhani wodziwika ndi kukanikiza mafunso.

Pocheza naye Msonda mu pulogalamu ya “Thumba la Tambe” pa Times, zinthu zidasintha kuchoka ku mafunso ndi mayankho abwinobwino kulowa ku nkhondo ya mawu koma ya wina ndi mzake.

Ken Msonda
Msonda: Anatengesana ndi Brian Banda.

A Msonda poyankha limodzi mwa funso adati iwo angathe kulipilira a Banda tikiti ya ndege kut akaone ku China komanso ku America popeza iwo azindikira kuti a Banda samayenda ndipo sakudziwa zomwe zikuchitika m’mayiko ena. Mtolankhaniyu anafunsa za komwe a Msonda atenga ndalama popeza amadziwika kuti ndi munthu oshota.

“A Msonda nthawi yomweyi mwazitenga kale kuti ndalama mukuti mundilipilire ine tikiti kupita ku America? Poti ine ndimakudziwani kuti ndinu oshota?” Banda adafunsa.

Poyankha funsoli a Msonda adanyuka kuti iwo ndi olemera kwambiri chifukwa adabweretsapo Lucky Dube kuno ku Malawi.

“A Brian ine ndinayamba ndabwera kudzadya kunyumba kwanu kapena kudzapempha kunyumba kwanu kuti mukanene kuti ndine osauka?” a Msonda adafunsa Banda.

“Ndipo ndati ndikuuzeni a Brian mwina simukudziwa, inu simukudziwa kuti Msonda ndi ndani ife ndi olemera mu thupi ndi muuzimu momwe, tachita zinthu zambiri mwina munali mwana simukudziwa. Mukudziwa kuti ndi ife tinabweretsa Lucky Dube mdziko muno, tinabweretsa Mbilia Bell,” adanyanyuka Msonda pokakamiza Banda kuti asinthe mafunso ake.

A Msonda adasintha kukhala osula atolankhani pamene adauza mtolankhaniyu kuti aziganiza za zinthu zothandiza ndi zoyenera kukhala nkhani. “Za umphawi wanga zipindulira bwanji anthu a mdziko muno? Chonde muziyang’ana zinthu zomwe zingapindulire mtundu wa a Malawi, munthu wa ku Chitipa apindula chani za umphawi wanga?” anayankha motelo a Msonda.

Pomwe Brian Banda adasintha kufunsa za tsogolo la a Msonda ku ndale iwo adati ndi Mulungu yekha amene amadziwa za tsogolo la munthu ndinso ndiye mwini anganene.

“A Brian musanabwere kudzamufunsa mafunso Msonda muzikonzeka, mudzisala kudya kwa sabata, taonani apa mwayaluka pa wayilesi,” Msonda adakwiya.

Pomaliza Banda adathokoza a Msonda chifukwa cha nthawi yawo, komanso adati iye sali odabwa kumva a Msonda akuyankha mwamwano komanso mwachipongwe ndi kuzemba mafunso ena chifukwa iwo adalowa nawo chipani cha DPP.

Advertisement