Zafika pano mzawo wa a Chaponda atha kukhala a Peter Mutharika okha ndi oyimba uja Joseph Nkasa.
Anthu otsatila chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) apempha mtsogoleri wa dziko lino amenenso ndi mtogoleri wawo a Peter Mutharika kuti amuvule unduna George Chaponda amene ndi nduna ya za malimidwe.
Malingana ndi chikalata chimene Malawi24 yaona chopita kwa mtsogoleri wa dziko lino kuchokera kwa anthu omukonda, iwo akupempha kuti a Mutharika achotse pa udindo a Chaponda.
“Ife ndi mzika zenizeni za DPP ndipo mukudziwa inu kuti sitinayambe takuponyanipo miyala,” alemba choncho mu chikalatamo kuuza a Mutharika.
“Akulu anu aja atatisiya, ife tinali nanu. Mayi Joyce Banda atakumangani, ife tinali nanu. Pa nthawi ya kampeni komanso ya zisankho, ifenso tinalipo. Ife timakonda chipanichi,” alemba chomwecho mu kalatamu kufuna kuonetsa kuti iwo ndi eni a chipani.
Anthuwo anenanso kuti ngakhale iwo ali okonda chipani motere, koma akhumudwa ndi mmene ikuyendera nkhani yokhudza nduna ya za ulimi a George Chaponda.
Iwo ati ali okwiya maka ndi kuti President Mutharika sakuchitapo kanthu pa ndunayi ngakhale bungwe lofufuza limene anakhazikitsa kuti lifufuze za kagulidwe ka chimanga ku Zambia linauza a Mutharika kuti a Chaponda akukhala ngati amafuna kuchita utambwali pogula chimanga.
“Bwana munalonjeza kuti muchitapo kanthu pa zimene bungwe limeneli lifufuze, apa labwela ndi zotsatila tikufuna muchitepo kanthu,” atelo mu kalatayo.
Iwo ati ngakhale akuvomeleza kuti Bambo Chaponda ndi msanamira wa chipanichi koma zafikapa madzi achita katondo ndipo palibe kuchitila mwina koma kumupitikitsa basi pa unduna.
Anthuwonso anena kuti a Chaponda akusokoneza zhipanichi chifukwa adani onse a chipani cha DPP ndi utosgoleri wa a Peter Mutharika akupezelapo mwayi onyoza kudzera mwa a Chaponda.
“Akutinyozetsatu mtaunimu Chapondayu. Adani athu a zipani zina, enanso obisalila mu mabungwe ndi ena onamizila kuti ndi atolankhani akupezelapo mwayi otinyoza,” atelo anthuwo.
71 thoughts on “A President, mukhiyeni Chaponda – atero anthu a DPP”
Comments are closed.










ndye mwat mutu wa nkhan nd,Mukhiyen chaponda kkkk koma kuwelenga nkhan yonse nd ku khiya sizifanana
Chaponda aphedwe basi
Nkasa wayaluka basi
ine ine zaunyani ine ndatopa ndi okuba aphunzitsi aphunzira aja adikilira ntchito osatenga ayiko chelete what for baibulo linati mutailanji ndalama ndi zinthu zosadya agaluwo anawelenga koma
ataninso achaponda? asova ndimomwe amadyela pano ali ziii agalu mwaona chaka cha 2018 azanamenso anyani
Nanga a Nkasa ndiye akuti chiyani tsopano. Poti amabakirawo ndi amene awonekera poyerawo