Inu nonse okonda kutsuka mkamwa ndi mau aululu, samalani tsopano. Lamulo likuchitani tintini.
Bambo wina wa zaka makumi atatu ndi mphambu zisanu ndi imodzi (36) wagamulidwa ndi bwalo la majisitireti mu boma la Machinga kuti akagwile ukaidi wa kalavula gaga kwa miyezi isanu ndi umodzi (6)chifukwa chotukwana.
Malinga ndi malipoti a Polisi, bamboyu a Lloyd Wazili ati anatukwana chikunja Mayi wina.
Ati bamboyu anapeza mayiyu atayima pa malo ena. Iye ati analonjela Mayi uja ndi mawu opempha kuti akagone naye. Koma mayiyu anakana ndi kumupempha kuti achoke.
Bambo Wazili mmalo moti achoke, ati anayamba kutukwana Mayi uja. Iwo anatchula ziwalo zobisika za Mayiyo ati chifukwa anakana kuti akagone nawo.
Bambo Wazili anagwilidwa ndi Anthu a zachitetezo a ku midzi amene anawauza a Polisi. A Polisi atabwela ndi kunjata Bambo Wazili, anachoka nawo chothawa ati chifukwa anzawo a Bambo Wazili amafuna kuthila makofi apolisiwo.
Ena mwa anzawo a Bambo otukwana mochititsa manyaziyu ati mpaka anatsatila ku Polisi komweko ati akamutulutse mzawo. Koma anagwidwa ndi kutsekeledwa.
Pa bwalo la Milandu, oweruza agamula a Wazili kuti akagwile kwa miyezi isanu ndi umodzi (6) kamba kotukwana pamene anzawo anayi amene anagwidwa akuti akatulutse a Wazili ku Polisi, awauza apeleke chindapusa.
116 thoughts on “Agamulidwa miyezi isanu ndi umodzi (6) chifukwa chotukwana”
Comments are closed.

I dedent wont conthises mutharika all presedent in malawi is wrong is asalantilly now live for god is seve pleblems hi she fogtern cocision only god can jug pleblems thank you
Ndatopa ndi kumva andale akuyankhula modzikudza nayenso mutharika akuyenjeza tinangobetsa mavoti athu njala ilimbwelekete ku malawi nanga tisankha ndani
Oba ndalama zachimanga nanga??
Send more police in our area tili ndi wa police m’modzi kuno kuti ayiyambe yomangawo amenyedwa
Nde zitinso izi? Malawi will never seize to be a laughing stalk. Malawi bomboclaat laws.
Guys nanga wakuba chimanga zaka zingati?
kkkkk ena akuba ndalama za LDF Osamumanga koma ukatukwana umangidwe? Malawi sadzatheka ndithum