Anaoneka udolo pa Kamuzu stadium ataitidzimula Nyasa Big Bullets. Anapitiliza udolo ku Lilongwe poimenyanso Nyasa. Koma a nyerere atha kugulitsilidwa bus imene anaipambana.
Malinga ndi malipoti amene tapeza, bus imene timu ya Wanderers inapambana mu mpikisano wa Bus ipite okonzedwa ndi a Luso TV ili pachiopsezo chogulitsidwa.

Malipoti anena kuti bus’yi imene inafikila ku galaja itatsala pang’ono kukhuthula osewela a nyerere cha mu Ntcheu umu yagwidwa ndi kampani yokonza ndi kugulitsa magalimoto ya Nissan.
Kampaniyi yagwila bus iyi kudikila kuti ikaomboledwe pa mtengo wa K1.2 miliyoni yomwe atchaja pa ntchito yomwe anagwila.
Padakali pano kuli chifwilimbwiti a Luso TV atakana kuti iwo salipila ndalama imeneyo.
“Ife sanatiuze kuti bus inaonongeka, sanatiuze zoti akukayikozetsa,” anatelo a Luso TV kwa atolankhani.
Nawo a nyerere akukana kulipila yoombolela ati poti bus inaonongeka a Luso TV asanamalize ndondomeko zowapatsila galulalo.
A kampani ya Nissan ati anena kuti ayamba kuonjezelapo chindapusa pa mtengo okonzelawo ngati bus ingachedwe kukatengedwa.
Malinga ndi Mkulu wina wa za malamulo, ndalama zoyenela kupelekedwa zikachedwa, a kampani ya Nissan atha kugulitsa bus kwa amene angaifune.
“Sangangopitiliza kuisunga, ikalakwa aigulitsa basi,” anatelo mkuluyo.
Zitha kutheka kuti mwina nawo a Bullets atha kuzapeza mwayi ogula bus imeneyo.
137 thoughts on “Bus inapambana nyerere ija mutha kuigula pompano”
Comments are closed.

mavuto anu ndi angati mwasowa zolemba eti bus imakuwawani asiyeni a noma pano akupuma zaaautsilu eti
Olo itagulitsidwa bola tinakuumbudzabe 5-1
akapado mumasowa zolemba etndakuonani ndinu ABB koma palibe chimene mungapange ndi ife anyelele mungotsata ganyu mukugwilayo osati nyasi mukulembazo
vry complicated sentence, mukakhaleso kacikena class only for chimangilizo, osati zomwe mwalemba apazi
Ur very stupid inu nonse a Malawi 24
Sindmadziwa kut Malawi 24 nd ya bullets… mwaitha!
Zooma kkkk
Shame to u this is sporting activities doesn’t make any sense to talk nonsense how could be done if anothe opponent worn that bonazza with that life u give unfortunate things to BB team and believe me the will never and ever win again any trophies here in malawi.lets wait and seee God is not your auncle you BiBi supporters shame to u
tinene kuti bus imeneyi ikupanga phokoso chifukwa choti inatengedwa ndi noma, kodi ikanatenga bullets bwenzi mukulembanso zotelezi, ngati munkadziwa zoti bus imeneyi ndi manyaka simunakane bwanji kusewera ndi noma, mtima ozikonda, munafinyidwa kawiri koma simukumvesesabe, komadi anthu inu ndinudi ma savage ndakhulupilira pano, inu ndamene mukupangisa kuti mpila uzilowa pansi ku malawi kuno, kuzolowera kubelekedwa. kumavomeleza agalu inu a news 24, musanyozese bullets apa…
Kodi kwanu nkuti jorno iwe???? Kamuzu stadium ndi nkhaniyi zikugwirizananji? Munthu onvesa chisoni…….mxieeeeew!!!!
Kma umbuliwu nde atiti agulitsa da last tym I remember its their bus n they have da right to do whatever they want to do with it
Klkkkkkkkkklkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkk chawanyelela chipako anoma bullets imalimbikila pa zinthu zaphindu osati za bus ayi.
Bus imawonekelatu kuti ndiyokutha mene umatulusila utsi wake ndiye anoma amawona ngati aphula imeneyo ipita pa mtengo wa 5 mita basi
Ndichifukwa timati News24 ndiina mwa Newspaper zodanitsa mdziko muno, nanga kulembako mkuti, omwe amadzitcha madolo zaonetseratu kuti iwowo sadasangalale kuwina kwa Noma.koma bullets siinafune kuluza kuja koma kulephera basi vuto lakwathu ndi msanje basi ndi Noma
Umbuz basi wakula anayamba abules kuluza
Malawi24 You Hv2 Evaluting B4 Post