Ku Lilongwe, mahule ayambitsa bungwe lawo ndipo asankha atsogoleri

prostitution malawi

Zosatheka zikutheka.

Ma lipoti akusonyeza kuti akazi oyendayenda amenenso amatchedwa kuti mahule apanga bungwe lawo. Amayiwa atinso asankha atsogoleri awo amene aonetsetse kuti bungweli likukua ndipo likhala ndi ma membala ambiri.

Malingana nsi malipoti amene tapeza, ati mayi Lucy Mtajili akhala mtsogoleri wag ulu limeneli limene akulitchula kuti Lilongwe Sex Workers Alliance. Mayi Mtajili ali ndi wachwili wawo amene ndi Chisomo Malichi.

sex-workers-newPamsonkhano umene anachita ma membala a gulu limeneli amene onse ndi amayi oyenda usiku, iwo anavotelanso mayi Caroline Makuwira kukhala Mlembi wa gululi pamene a Angella Tchauya akhala wachiwili.

Msungichuma wa gululi ati asankha kuti akhale Mayi Violet Banda amene wachiwiri wawo ndi Mayi Kelia Banda.

Pakhala pakukambidwa manong’onong’o oti amayi oyenda usiku akufuna ufulu wawo uzilemekezedwa. Ena akhala akupempha kuti ntchito yawo ikuyenela kuvomelezedwa ndi a boma ati cholinga choti azitetezedwa ku nkhanza zimene amakumana nazo usiku kuchoka kwa owagula komanso apolisi.

Ngakhale zili chonchi, a Malawi ena akuoneka osasangalala ndi khalidwe lotere ndipo akhumudwa ndi kupangidwa kwa bungweli ati chifukwa akuona kuti zikolezela uhule.

Advertisement

6 Comments

  1. Nde shani ishi…iyaaaa

    Kwanilitsani malembawo koma tsoka kwa iwo okwanilitsa zomwe zinalembedwa

  2. Oh my God!!!

    These are the last days, in the last days people will be boasters and proud. Pride is the cause of Satan’s fall because he wanted to be exalted above God and the world today is full of proud and boastful people. Watch out!! Dziko likutha ili.

  3. Bungwelo lalembetsedwa kuboma? Likulu lilikt? Kutha kwadzko, ISAIAH talked of dem, women of Jerusalem,,,,

Comments are closed.