A Malawi alibenso chikhulupiliro mwa a Mutharika, ati bola a Chakwera

Advertisement
Peter Mutharika

Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika akuyenela kukhala ndi mantha.

Peter Mutharika
A Mutharika mbiri yawo ‘yaipa’.

Malinga ndi kafukufuku wa Bungwe la Centre for Media Development (CMD) ati anthu ambiri mu dziko muno ataya chikhulupiliro chawo mwa a Mutharika.

Kafukufuku ameneyu ati wapeza kuti mmalo mwa a Mutharika, a Malawi akuona kuti mtsogoleri otsutsa Boma a Lazarus Chakwera ndiwo ali ndi kuthekela kopititsa dziko lino patsogolo.

Ati a Malawi akuona kuti a Chakwera ali ndi kuthekela kothetsa katangale, kuyambitsa chitukuko ndi kukonza ubale ndi maiko ndi mabungwe othandiza Malawi.

Koma kafukufuku ameneyu wathilidwa kale mphepo ndi a Malawi ena.

A Undule Mwakasungula amene anakhala akumenyela ufulu pa nthawi imene a Bingu wa Mutharika anavuta anena kuti zimene akukamba kafukufuku ameneyu ndi mbwelela.

“Anafunsa ndani, wakuti, anagwilitsa njira zanji?” anadabwa choncho a Mwakasungula.

Advertisement

2 Comments

  1. Palibe wandale amene alibwino mavuto awa sadayambe lero kulowa ndale kumalawi mkulinga ukuziwa ufiti (kukwima )

Comments are closed.