A mathanyula agwidwa masana, khoti liwagamula apeleke chindapusa

Advertisement

Bwalo la majisitileti mu mzinda wa Lilongwe lalamula amuna awiri kuti apeleke chindapusa chokwana K100, 000 atapezeleledwa akugonana mu galimoto.

Malinga ndi malipoti, amuna awiriwa anatanganidwa kugonana dzuwa likuswa mtengo. Iwo amachita izi mu galimoto.

Apolisi ati podabwa ndi manjenjemeledwe a galimoto, anapezelera awiriwa. Iwo anawamanga ndi kuwatengela ku Bwalo la majisitileti.

Chodabwitsa, awiriwa anayimbidwa mlandu ofuna kudzetsa chisokonezo mmalo moti ayimbidwe mlandu wa mathanyula umene amayenela kukasewenza jere kwa zaka khumi ndi zinayi.

Awiriwa anapezeka olakwa ndipo alamulidwa kuti alipile K50, 000 aliyense. Chigamulo chimene chapsetsa mitima a Malawi ochuluka pa Fesibuku.

Awiriwa ndi a Kelvin Gonani amene anamenyedwapo mu mzinda omwewo wa Lilongwe pa nkhani yokhudza mathanyula. Iwo anapezeleledwa ali ndi a Dave Luke.

Advertisement