Maule abela osewela awo ndalama

Nyasa Big Bullets

Mwina bola akanabela osewela a nyerere zikanamveka. Koma ayi ndithu chipongwe achita osewela awo omwe.

Ife a Malawi24 tapeza umboni oti anthu ena ochemelela timu yampira ya Nyasa Big Bullets adasolola ndalama zimene zimayenela kupita kwa osewela mpira a timuyo.

Malinga ndi nkhani imene tapeza, anthu ena okonda timu yampira ya Bullets anapanga gulu pa Whatsapp lomwe limatchedwa Big Bullets Sports News.

Nyasa Big Bullets
Osewera a Bullets akubeledwa mwa chibisira.

Pa gululi, anthu anagwilizana zoti asonkhe ndalama zothandizila osewela a timu yawo. Koma anthu aja atasonkha ndalama zija, ati sizinafike kwa osewelawo.

Anthu atatu amene amayang’anila gululo ati anaponda osewela awo omwendalamazokwana K300,000.

Ife a Malawi24 tapeza kuti m’modzimwaoyang’anilagululo a ChazamaMoyo anaba ndalama yokwana K100,000.

Ati ndalamayo anthu anasonkha kuti akagule mphatso yopeleka ku ukwati wagoloboyiwatimuyo, a Ernest Kakhobwe.

Anthu atazindikila kuti a Chazama asololandalama, anayamba kuwafufuza koma anamva kuti athawilaku South Africa.

Mkuluwina Hastings Chambuluka ati naye watchuka ndikuba ku gululi. Zapezeka kuti mkuluyu anaponda ndalama chakachatha zimene amayenela kuthandizila malemu Douglas Chirambo. Ati ulendo uno naye waba K50,000 imene imayenela kupita kwa osewela a timuyawo.

Kubaku sikunasiye malo pamene mayi wina, a Shazia Chelewani akuyimbidwa mulandu okuba K122,000.

Pamene tinayesela kufunsa onse oimbidwa mlanduwa kuba, iwo anakana kuthililapo ndemanga.

Advertisement