Chakwera ndi m’farisi – atelo a Boma

2

A Boma komanso a chipani cholamula atopa naye mtsogoleri wa Kongeresi Lazarus Chakwera moti ayamba kumuvula pagulu.

Lazarus Chakwera.

Chakwera: Wasambwazidwa!

Akulualuku a chipani cholamula cha DPP anamemeza atolankhani mu mzinda wa Lilongwe pamene anayamba kumumasula mtsogoleri wa zipani zotsutsa Boma mu nyumba ya malamulo.

“A Chakwera asamayankhule ngati mngelo,” anatelo a Francis Kasaila pa msonkhanowo.

“Iwo akunena Boma kuti likuononga ndalama, koma pompano amatipempha ati tiwagulile kanema azionela ku ofesi yawo. Ngati akukonda a Malawi sakanaona kuti kanema ilibe ntchito pamene anthu akuvutika?”

A Kasaila anaonjezelanso kunenapo kuti Boma la a Mutharika lili pakalikiliki kuonetsetsa kuti njala isaphe anthu m’dziko muno, zinthu zimene a Chakwera anawadzudzula a Mutharika kuti amalephera.

“Tagula chimanga kuchoka ku Mexico ndi ku Zambia, cholinga anthu asafe ndi njala, ndiye a Chakwera akuti chani kwenikweni?”

A Kasaila analangizanso kuti a Chakwera asamangotsutsa chilichonse ndipo asiye kukhumbila mpando wa a Mutharika.

A Chakwera anaputa mavu a DPP atanena kuti Boma la a Mutharika lalephela kutukula miyoyo ya a Malawi.

Atanena izi, nduna ya zofalitsa nkhani pa nthawiyo a Malison Ndau analemba kalata yamnyozo kutonza a Chakwera. Koma kalata ija isanathe kuwanda Malawi yonse, a Mutharika anachotsa ntchito a Ndau.

Share.

2 Comments

%d bloggers like this: