Mayi amangidwa kamba kogwilira bambo

220

Apolisi mu boma la Machinga ananjata mayi wina wa zaka makumi awiri ndi mphambu zisanu ndi imodzi (26) ati kamba kogwlira bambo wina wa zaka makumi awiri ndi mphambu zitatu (22).

Malinga ndi mneneri wa a Polisi mu boma la Machinga, mu mwezi wa Okotobala chaka chomwe chino, Mayi Inness Salamba ati anagwililira bamboyu.

SexIwo anati Mayi Salamba anaitanila bamboyu kunyumba kwawo, ndipo atafika kumeneko iwo anavula ndi kumukakamiza kuti agone naye.

Ati bamboyu atapita kwawo anaoneka otopa ndi osokonezeka ndipo atafunsidwa, iye anaulula kuti wachitidwa chipongwe ndi mayiyu.

Apa akuti achibale a bamboyu anakaitula nkhani kwa amfumu amene ananena kuti nkhaniyi apite nayo ku Polisi.

Atamva zoti nkhani yakatulidwa ku Polisi, ati Mayi Salamba anathawa osaonekanso.

Iwo anaonekanso mwezi uno poganiza kuti nkhani ija yaola, koma anangofikila mmanja mwa a Polisi.

Iwo atengeledwa ku bwalo la milandu posachedwapa kukayankha mlandu ogwililira ndipo akapezeka olakwa atha kukakhala kundende kwa zaka zisanu ndi ziwiri (7).

Share.
  • Opinion