16 November 2016 Last updated at: 10:33 AM

Zanu zimenezo: boma linyanyala a Malawi ogwidwa mu dziko la South Africa

A Malawi onse amene anagwidwa mu dziko la South Africa kamba kopita mu dzikomo opanda chilolezo ndipo akusungidwa pa malo a Lindela kudikila kubwela mu dziko lino ayiwale kuti abwela msanga.

Izi zadziwika pamene a boma anena kuti alibe ndalama zokawatenga a Malawi amene akusungidwa ku malo a Lindela.

Lindela RSA

Malawians at Lindela will not be helped.

“Mu ndondomeko ya boma ya chaka chino munalibe ma dongosolo amenewo, ndipo boma likuvutika kupeza ndalama. Silingaseweletse ndalama kukawatenga anthu amenewo,” anatelo mkulu wina ogwila ku unduna woona za maubale ndi maiko ena.

Mkuluyu anaulula kwa Malawi24 kuti a boma aganiza zoleka kutenga a Malawi amene anagwidwa mu dziko la South Africa ati Kamba izi zikuthela dziko lino ndalama.

Koma poyankhulapo, nduna yoona za maubale ndi maiko ena, a Francis Kasaila, anati pa lamulo boma la Malawi silikuyenela kukawatenga a Malawi kumeneko.

“Si ife tinawagwila, linawagwila ndi dziko la South Africa. Amene anawagwilawo ndi amene akuyenela kuti athandize anthu otelewa kubwelela kwawo,” anatelo a Kasaila.

Iwo anaonjezelapo kuti malamulo a pa dziko lapansi amafotokoza momveka kuti dziko limene lagwila anthu ndilo likuyenela kuwatumiza kwawo.

Amalawi oposa chikwi (1000) akusungidwa pa malo a Lindela amene anthu amanena kuti amakhala ngati ndende ndipo kuli nkhanza zosiyanasiyana kuphatikizapo kumenyedwa.480 Comments On "Zanu zimenezo: boma linyanyala a Malawi ogwidwa mu dziko la South Africa"

Leave a Reply