9 November 2016 Last updated at: 12:07 PM

A Malawi apemphedwa kuti azilola amayi kuchotsa mimba

A Malawi apemphedwa kuti akhale anthu omvetsetsa pa nkhani ya lamulo lokhudzana ndi kuchotsa mimba.

Malamulo ololeza kuchotsa pakati akufunika ku Malawi.

Malamulo ololeza kuchotsa pakati akufunika ku Malawi.

Malingana ndi mkulu wa bungwe loona kuti palibe kusiyana pakati pa akazi ndi amuna, la Gender Coordination Network, Mayi Emma Kaliya, a Malawi akuyenela kukhala anthu olola kuti lamulo limeneli liikidwe.

Pakhala pali mpungwepungwe pakati pa a Malawi pamene ena akufuna kuti amayi aziloledwa kuchotsa mimba koma ena, maka atsogoleri a mipingo akukana kuti ayi. Iwo ati chifukwa kuchotsa mimba ndi kupha.

Koma onse ogwilizana ndi kulola kuti amayi azichotsa mimba ati dziko silingamalamulidwe ndi malamulo a Chalichi. Enanso akuti mchitidwe ochotsa mimba umachitika ndi kale koma mwa njira zosayenelela.

“A Malawi akuyenela kugwilizana ndi lamulo lovomela kuchotsa mimba ili kuti titeze amayi ndi asungwana amene akufa Kamba kochotsa pakati,” anatelo a Kaliya.

A Phungu a kunyumba ya malamulo akuyembekezeka kukambilana za nkhaniyi.

 246 Comments On "A Malawi apemphedwa kuti azilola amayi kuchotsa mimba"

Leave a Reply