1 November 2016 Last updated at: 2:31 PM

Mnyamata wa ku Chanco akomoka pa chisembwele

Kunali chipwilikiti ku sukulu ya ukachenjede ya Chancellor ku Zomba zitamveka kuti ophunzila wina wapasukuluyo anakomoka ali mkati mochita za chisembwele ndi msungwana wina.

SexMalingana ndi ma lipoti amene talandila, ati mnyamatayu anapita mu chipinda cha mtsikanayu kuti akachite ntchito za kwaipa. Koma ali mkati mochita ntchito za kwaipa kapena kuti kuionetsa monga akunenela anyamata amakono, iye anakomoka.

Apa akuti zinamuopsa msungwanayu ndipo iye anayamba kukuwa kuyesa kuti mnayamatayo wafa.

Anthu atakhamukila kumaloko kuti akaone chimene chinali kuchitika, anapeza mnyamatayo ali kwala pa kama wa msungwanayo, ali chibadwile. Ena ati anali atavala ka chishango kozitetezela.

Atamuunika anapeza kuti iye sanasiye kupuma iyayi koma anali chabe okomoka.556 Comments On "Mnyamata wa ku Chanco akomoka pa chisembwele"