26 October 2016 Last updated at: 10:20 AM

A Malawi akwiya ndikuletsedwa kwa chakumwa cha Frozy

A Malawi ambiri ati ndiokwiya ndikulesedwa kwa chakumwa chozizilitsa kukhosi cha mdziko la Mozambiki cha Frozy.

Kukwiyaku kukutsatira zomwe lanena bungwe lo unika zinthu mdziko muno la Malawi Bureau of Standard (MBS) dzulo pa 25 Okutobala kuti chakumwachi ndicholetsedwa mdiko muno.

Bungwe la MBS lati mumchakumwamu muli tizinthu tina tomwe sitikuenera kukhala muzakumwa ndipo izi zapangisa bungweri kuti liletse chakumwachi.

frozy

Chakumwa cha Frozy chaletsedwa.

Mwazina bungweri lati lizipereka chilango kwaonse opezeka akumwa komaso kugulitsa chakumwachi, ndipo izi zakwiyitsa anthu ambiri mdziko muno.

Poyankhapo pankhaniyi yomwe inaikidwa patsamba la nyuzipepala ino dzulo, anthu ambiri ati izi ndizoduka mutu.

Iwo atiakuganiza kuti bungweri latumidwa ndi kampani yopanga zakumwa ya Carlsberg kuti alaletsa chakumwachi kamba koti kubwera kwa chakumwachi kwapangitsa kuti malonda azakumwa monga fanta komaso kokakola avute.

Mmodzi mwaotsatila nyuzipepala ino a Steve Mumbulu anati “MUKULESA FROZY PAMENE FANTA WAKUMALAWI NDIWOKWELA MTENGO NGATI MADZI OPANGILA MUMACHITA KUWODETSA KUNJA.MADZI OKHA MPAKA K250 PAMENE FRONZY K2OO NDI BOTTLE LOMWE. ZOKUMWA ZAKUMALAWI NDI ZODULA KOMANSO ZOSAKOMA.TAX YACHANI PAMENE NDALAMA ZA TAX ZINGOBEDWA IFE TIZILIPILA NSOKHO INU MUZIBA FROZY NDI DHIL NDIPO MUPANGE MA 1LITRE TIZIMWA BASI NDALAMA NDI ZANTHU..”

Anthu ena adzudzula bungweri kuti bwanji likulora mowa ochokera ku Mozambiki konko kumagulitsidwa kuno kwathu ku Malawi ndipo ena anaonjezera kunena kuti frozy asaletsedwe chifukwa sanachotsepo moyo wamunthu komaso palibe banja lomwe wathetsa.

“Ndimabanja angati omwe frozy wathetsa, ndimoyo ingati yomwe wachotsa? Bwanji nanga sikuletsa zakumwa zoledzeletsa monga mkalabongo, sibwino. ” anatero a Mary Chatha.

A Frank R Meleka anati ilindiganizo labwino ndipo anaonjezera kuti “KOMA ANTHU ENA NDINUDI AMALAWI KOMA? INU MUKUKHALA NGATI ANTHU OSAPHUNZIRA BWANJI ,JUST GO TO TZ ZAMBIA IF YOU CAN GAT A PRODUCT YA SUN CRAEST ,KUNGOPEZEKA AMAKUFUSA MAFUSO OVUTA KUYANKHA WACHOKA NAZO KT ZIMENEZI KUNO AYI,KOMA IFE KUNO TIMANGOLANDIRA ZILIZONSE.

Mwa anthu 500 oyambilira omwe anaikilapo ndemanga pankhaniyi, anthu 487 anati ndiokwiya ndi kuletsedwaku pamene anthu 7 anayankhula zosagwilizana ndinkhaniyi ndipo folo otsalawo ati kuletsedwaku ndikwabwino kwambiri.341 Comments On "A Malawi akwiya ndikuletsedwa kwa chakumwa cha Frozy"