Mtsogoleri wakale wa dziko lino a Bakili Muluzi wati ndiokhumudwa ndi imfa ya mkhala kale pa ndale a Gwanda Chakwamba.
A Chakwamba amwalira dzulo pa 24 Okutobala masana pachipatala cha Blantyre Adventist mu mzinda omwewo wa Blantyre atadwala kwakanthawi kochepa.
Sabata latha nyuzipepala ino inakupasilani nkhani kukudziwitsani zakudwala kwa malemuwa omwe amadwala nthenda ya mtima ndipo anagonekedwa pachipatalapo mpaka dzulo pomwe atisiya.

Poyankhulapo pa zaimfayi, mtsogoleri wakale wadziko lino a Muluzi omweso anagwirapo ntchito ndi a Chakwamba, ati ndiokhumudwa kwambiri ndiimfayi.
Muluzi wati adzawakumbukila malemuwa ngati munthu olimbikira komaso osabwelera mmbuyo akafuna kupanga zinthu ndiposo opanda mantha.
“Ndinauzidwa kuti Gwanda wamwalira. Ndimadziwa zoti anali kuchipatala ku Blantyre koma ndimaganiza kuti akhala bwino ndipo nditava za imfa yawo ndamva chisoni komaso ndakhumudwa kwambiri.
Chisoni chikubwera chifukwa ndinawadziwa a Chakwamba zambirimbiri zapitazo, enafe tili anyamata tikuyamba kumene ndale. Tinagwilira ntchito limodzi mu mchipani cha MCP komaso cha UDF ndipo ndikufuna ndipepese kwambiri kumtundu wa a Malawi kamba ka imfayi” wadandaula Muluzi.
Mogwirizana ndi a Muluzi, mtsogoleri wakale wa chipani cha MCP a John Tembo, nawoso ati imfa ya Chakwamba yawakhudza kwambiri.
A Tembo ati ngakhale ndi a Chakwamba nthawi zina samagwirizana, koma malemuwa anali olimbikira pa ndale ndiposo mumchipani komaso amadziwa chomwe amapanga ngati namandwa pa ndale.
A Gwanda Chakwamba amwalira ali Ndizaka 82 ndipo anabadwa pa 4 Epulo 1934 ndipo wasiya mkazi, ana atatu, zidzukulu zitatu komaso zidzukulu tudzi zinayi.
109 thoughts on “Bakili, Tembo akhumudwa ndi imfa ya Chakwamba”
Comments are closed.


Chakwamba pa 17 may 1973 ndi amene anamenya mafumu ku nzuzu kuwatibula ameneyo angakhale pulezidenti anatero a tcheya
Rest in peace.
Obvious
nzimu wa gwanda use mtendere ameni
Assaaa asatinamizepo apa nkhani ndi nkhawa kuti who wanner be the next
Choti anthu inu muziwe musiyanise nthawi yaka mpeni ndiya imfa ndi zithu ziwiri zosiyana anthu nthawi yakampeni amayankhula zandale cholinga awine kumbali yawo koma akachoka pa msonkhano anthu aja amagwirizana palibe cholakwika Tempo & Bakili chifukwa si nthawi yandale inu ngati muli mbuli pa ndale ndichifukwa chake mukuyankhula kuti Bakili &Tembo asayankhulepo kathu ndiwe mbuli pandale ndale siwudani ayi mbuzi ya munthu iwe asiyeni anthu akhuze maliro
May soul rest in eternal uncle
Amati azikhalabe moyo mpakana ku?.asampanse minyama Gwanda.siyeni kut naye akapume ndi angelo
Amen!may his soul rest in peace in Jesus name!
Rip mbuya mwana zwele nkhabe wamuyaya tayi
Amalawi tiyeni tisiyanise ndale ndi imfa chodandaulisa ena akunyoza why munthu amamvera chisoni munthu nzake tiyeni tikhudzike ngati amalawi
Rip mbuya mwana zwele nkhabe wamuyaya tayi
Rip mbuya mwana zwele nkhabe wamuyaya tayi
Rip mbuya mwana zwele nkhabe wamuyaya tayi
Mchiyan kod amalawi tidzasiya liti kunyozana nduthenga wamalilo womwe o malawi tikadavutika
Bakile wati wachita bwanji ndi imfa ya Chakuamba? Koma anthufe mulungu azingotikhululukira. Chomwe timayankhula nthawi zina sitimachidziwa, zomvetsa chisoni kwambiri.
Kodi mukamati Mtsongoleri wa kale wadziko lino mukukutathauzanji? Poti ena amene akuwelenga nkhaniyi ali kumaiko akunja. Ndiye adziti Dziko lake liti pofuna kuitsata nkhaniyi?
You are very much aware that the post you are commenting on is Malawi 24 .
Chakuwamba pa 17 septmber 1972 ndiamene anamenya makofi mafumu okwana 19 kwa achikula including amfumu achikumbu ndan sakuziwa bwino. Muse mumtendele madala zimachitika
bakili ndiwabodza suja amkati chakwamba ndimunthu oyipa nde lero chisonicho chilipati
paumunthu ayenela kutelo takumbukilini pakati abingu ndi abakili zinali bwanji? koma kumwalira kwa abingu abakili anakhala nawo zimasiyana ndichidani cholimbilana ufumu wa pamudzi chimakhala chamutima koma zandale zimakhala zanthawi yomweyo akulimbanayo zikatha amayambaso kumwela limodzi inu kutsala tikulumana zopanda tchito