25 October 2016 Last updated at: 3:13 PM

Bakili, Tembo akhumudwa ndi imfa ya Chakwamba

Mtsogoleri wakale wa dziko lino a Bakili Muluzi wati ndiokhumudwa ndi imfa ya mkhala kale pa ndale a Gwanda Chakwamba.

A Chakwamba amwalira dzulo pa 24 Okutobala masana pachipatala cha Blantyre Adventist mu mzinda omwewo wa Blantyre atadwala kwakanthawi kochepa.

Sabata latha nyuzipepala ino inakupasilani nkhani kukudziwitsani zakudwala kwa malemuwa omwe amadwala nthenda ya mtima ndipo anagonekedwa pachipatalapo mpaka dzulo pomwe atisiya.

Gwanda Chakuamba

Gwanda Chakuamba: Adatisiya dzulo.

Poyankhulapo pa zaimfayi, mtsogoleri wakale wadziko lino a Muluzi omweso anagwirapo ntchito ndi a Chakwamba, ati ndiokhumudwa kwambiri ndiimfayi.

Muluzi wati adzawakumbukila malemuwa ngati munthu olimbikira komaso osabwelera mmbuyo akafuna kupanga zinthu ndiposo opanda mantha.

“Ndinauzidwa kuti Gwanda wamwalira. Ndimadziwa zoti anali kuchipatala ku Blantyre koma ndimaganiza kuti akhala bwino ndipo nditava za imfa yawo ndamva chisoni komaso ndakhumudwa kwambiri.

Chisoni chikubwera chifukwa ndinawadziwa a Chakwamba zambirimbiri zapitazo, enafe tili anyamata tikuyamba kumene ndale. Tinagwilira ntchito limodzi mu mchipani cha MCP komaso cha UDF ndipo ndikufuna ndipepese kwambiri kumtundu wa a Malawi kamba ka imfayi” wadandaula Muluzi.

Mogwirizana ndi a Muluzi, mtsogoleri wakale wa chipani cha MCP a John Tembo, nawoso ati imfa ya Chakwamba yawakhudza kwambiri.

A Tembo ati ngakhale ndi a Chakwamba nthawi zina samagwirizana, koma malemuwa anali olimbikira pa ndale ndiposo mumchipani komaso amadziwa chomwe amapanga ngati namandwa pa ndale.

A Gwanda Chakwamba amwalira ali Ndizaka 82 ndipo anabadwa pa 4 Epulo 1934 ndipo wasiya mkazi, ana atatu, zidzukulu zitatu komaso zidzukulu tudzi zinayi.109 Comments On "Bakili, Tembo akhumudwa ndi imfa ya Chakwamba"