
Nduna yoona zofalitsa nkhani imenenso ili mneneri wa boma a Malison Ndau auza atolankhani ndi mabungwe ena amene amafuna kuti iwo apepese ati kamba koti ananena bodza pa za umoyo wa mtsogoleri wa dziko lino kuti iwo sangapepese.
Mabungwe ena omwe si a boma anakhala akuyimba milandu a Ndau kuti apepese pouza mtundu wa a Malawi kuti a Peter Mutharika ali ndi moyo wangwiro ku Amereka. Koma a Mutharika atabwela ananena kuti io nyamakazi inawasautsa ku Amereka kutanthauza kuti amadwala.
Koma poyankhulapo pa nkhaniyi, a Ndau amene amanenela boma ndipo anaopseza kuti anjata anthu amene anali kutchukitsa kuti a Mutharika anali akudwala anayankhula kuti sangapepese.

“Ine sindinaname iyayi, ine ndimanenela boma ndipo ndinanena zimene a boma amadziwa. Ku boma timadziwa kuti a Mutharika ali wangwiro ndipo sitinaname konse,” anatero a Ndau.
“Choyenela kudziwa ndi choti a Mutharika ali ndi moyo wawo umene pena umayenda opanda a ku boma kudziwa, nkhani ya matenda iyi sitinauzidwe poti sanali matenda enieni,” anaonjezelapo a Ndau.
A mabungwe anapsela mtima a Ndau ati chifukwa ananena kuti Mutharika ndi wangwiro koma mwini wache ananena za nyamakazi. Koma ngakhale zili choncho, a Mutharika ananena kuti nyamakazi imene inawavuta sinali vuto kwenikweni.
“Kanali chabe ka nyamakazi kamene kanavuta, ndipo ine ndikudziwa palibe munthu anafapo ndi nyamakazi kupatula mwina ku Zodiak,” anatelo a Mutharika polankhula ndi atolankhani lachisanu.
A Mutharika anakhala ku dziko la Amereka misonkhano imene anapitila itatha. Iwo anaonjezela kukhala kwawo ndi masabata awiri. Izi zinapangitsa anthu kuyamba kufalitsa nkhani.
Zinatchukitsidwa kuti a Mutharika akudwala. Iwo atabwela mdziko muno anaonjezela mphekesela izi pokanika kugwilitsa ntchito mkono wawo ma dzanja la manja.
94 thoughts on “Sindipepesa – atero a Ndau pokhudzana ndi matenda a Mutharika”
Comments are closed.


Tizingomphempherelana
Olo asapepese idon,t care
Kikikikikikiki!wat a governmnt,apology 4 wat?kudwala ndi kudwala basi.so he thnk he z so strong,apology nt needed at all
Kkkkkkkkkkkk akapepesa ndiye mutani?kufuna ulemu basi, muuze akwanu akupepeseni
Ukukana kupepesa ngati ndani iweo? koma ukutidziwa bwino bwino kuti ndife ayani?uona polekera come 2019 khala choncho usapepese!
Ukufuna akapepesa ndiye utanino iweo
Palibe chomwe ndingapange atapepesa,koma nkhani ndiyakuti ali kumeneko kutumikira ife a malawi,nde asamabise chinachilichonse chizikhala poyera tonsefe ndife amodzi nde that guy akuyenera kapepesa ku mtundu wa a malawi chifukwa chosanena zithu zoona.
Apepesa bwanji munthu amauza mtundu wa a malawi zomwe DPP govt inamutuma.
Tizaona ngat suzapepesa 2019
Tizaona ngat suzapepesa 2019
Tizaona ngat suzapepesa 2019
andalewa kungowasiya sakuva madandaulo ayife koma thawi yovota timafunika
Dzimenedzo ndiye mdzauchitsilu,kodi nkulu wako uja alikuti? Ngati adapita iyeyo nangaiwe ndiye ndani?kodi ukuganidzakuti ungadziombole ndi chuma chako?chibwana chimenecho,mulungu wakuchilitsani kuti mube komaliza akubwela adzakutengeni,ngati nthawi yakwana palibe kupsatila,payele payele basi,kapumeni mwaba mokwanila,
Ngati umatha kolodza anthu akwani president siwakwanu anthu agule iwe
Iwe ukunena mozitama ngati suzafa? uyambe wafunsa anthu akwanu kuti abale ako ena ali kuti before kulankhula moputsa chomcho wamva #James nkhumba yamunthu iwe. Ndipo uyambe kufa ndi iweyo before APM
Iwe Nkanda choyamba ndikuti panyopako, ngati umalodza anthu ndikwanukomweko mfiti iwe. Ukuwona ngati kuti iye atamwalira angavutike maikidwe, ameneyu dziko lonse kuziwa kusiyana ndi mphawi ngati iwe odya zotoleza ngati nkhumba. Uwona, ufa ndi cholera akubwera posachedwapa tione ngati anthu angamve zoti fisi winawake wamwalira. Usazayambilenso kulankhula mopusa, panyopako basi ndapita ndikukagona uyetse kuzanditambira ndikutchola pomwepo.
KKKKKK kkkkkkkk zivele wekha fan pirta ok
Mwina akuziona ngati chitsulo. Palibe kupepesa PETER ndi odwara basi, olo zibagera sangalimbe nazo. Wa miyoyo nine amaliliranso kupepetsedwa utsilu eti?, mwaiwara kuti manda aja akutidikira a moyofe. Utsogoleri muzawasiyira ena ku dziko kuno akulamulira iwe{peter} uzapita ulibe kali konse.
Koma ameneyu! amayenera kupepesa basi. Kodi iyeu mese ndi mbusa? Kapena ndiwasataniki eti?
Ukayambe wafusa chakwela kt anali ndani asana bwere ku ndale
Anthu a kugona mu mdima wopanda magetsi anayamba wapepesa who is he to people If he is failure to deliver even little thing to Malawian citizen shame on you
Ukadwala ikhala nkhaniso.Mulungu amaona sungabitse chinachilichonse.sungabitse matenda pamene ukudwala.Tithokoze Poti Chauta Anatipatsa Moyo.Anthufe timatenga moyo ngati wathu mwini wake alipo.moyo 2 sagula ngakhale ukhale ndindalama zochuluka bwanj sungagule moyo.Heart is a precious
that’s why i don’t support any political party,
Kaya Zawo Izo
Zinavuta anzanu izo
Mutharika ananena pa press conference kuti if there is any1 to blame is him,not mgeme or Ndau.ma journalist aku Malawi simumamva olo pang’ ono.APM is the 1 to apologize not ndau or mgeme,koma mukumuopa that’s y mukulimbana ndi mgeme.