22 October 2016 Last updated at: 8:34 AM

Mutharika asambwaza Chakwera: Thana kaye ndi mavuto a mu Kongeresi kenako undilangize ine 

Peter Mutharika and Lazarus Chakwera

Mutharika (L) wathila mphepo Chakwera (R). (File)

Zimene analankhula mtsogoleri wa chipani cha Kongeresi, a Lazarus Chakwera, pa msonkhano ku Dedza kutha kwa sabata latha zawapezetsa mavuto pamene mtsogoleri wa dziko lino amene naye ali mtsogoleri wa chipani cha DPP, a Peter Mutharika, anaganiza zowayankha lachisanu.

A Mutharika amene amalankhula kwa atolankhani dzulo, anapezelapo mpata oyankha a Chakwera.

“Wina amati nditule pansi udindo wanga, osakonza kaye mavuto ali mchipani chako bwanji usanandiuze ine zimenezo?” anatelo a Mutharika.

A Chakwera anati a Mutharika atule pansi udindo wawo ati kamba dziko lino limakumana ndi mavuto a mnanu kunkhani ya umoyo wa anthu komanso ya zachuma.

Mmene a Chakwera amanena izi ndi kuti a Mutharika asanafike mu dziko muno, ali ku Amereka komwe anthu anatchukitsa kuti akufuna thandizo la mankhwala koma eni ake atsutsa izi dzulo ati ponena kuti iwo samafuna thandizo la mankhwala koma anali pakalikiliki osaka mwayi wa a Malawi.

A Mutharika dzulo anachiona choyenela kuyankha mkulu mzawo a Chakwera.309 Comments On "Mutharika asambwaza Chakwera: Thana kaye ndi mavuto a mu Kongeresi kenako undilangize ine "