A Mutharika mwina ayankhula kwa a Malawi lero


Peter Mutharika

Pataphulika mphekesera zoti mtsogoleri wa dziko lino anachedwa mu dziko la Amereka kamba koti anagonekedwa ku chipatala, mkuluyu ali ndi mwai otsitsa nkhani zimenezo lero mwa yekha.

Malingana ndi a kunyumba ya boma ku Lilongwe, mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika lero akhala akuyankhula ndi atolankhani.

A kunyumba ya boma ati a Mutharika alankhulana ndi a tolankhani lero zokhudza ulendo wake wa ku Amereka koamnso nkhani zina.

A kunyumba yaboma ati atolankhani oposera makumi anayi aonetsa kale chidwi chofuna kumva mtsogoleri wa dziko lino.

“A President akumana ndi atolankhani lachisanu, pa 21 Okotoba,” anatero mneneri wa a President a Mgeme Kalirani.

Anthu ambiri akhla tcheru kumva a Mutharika kamba koti atafika mdziko muno sanalankhulepo ngakhale liwu limodzi ndipo anli okanika kugwiritsa ntchito mkono wawo wa dzanja lamanja.

Atafika anthu amene anali ndi chikayiko kuti mdziko la Amereka mkuluyu amadwala, anavomeleza ataona mmene anakanikila kugwilitsa ntchito mkono wa kumanja.

134 thoughts on “A Mutharika mwina ayankhula kwa a Malawi lero”

  1. Nkhan imeneyo yundinyasa kwambili kaya akudwala kaya sakudwala azidziwa yekha mukubisa matenda chinachake chikachitika tidzava.

  2. Kkkkkkkkkkkk ptar akumana nazo relo matenda mbali akathana akutikomweko ndi soja.lusiyasi banda ndiposo wadelela akutiso sakuopa anaziyambila kalekale thaw ya kamuzu ngati anamulephela akuakulu thaw imeneyo Nde unyundendani. ..bajatu musamuiwale lusias amafusa pakana muthu yemwe akumufusayo pakana kumwalilandi Bp ndinafuso

  3. madala. Mwavelanokho ana anuwa akukhalangati akukunyozani km ayisichocho kukudandawulila ndimene dzikolathu likuyendala. Chonde tayesesani kubwelapoyela ndikuwuza thundu waamalawi chowonachenicheni titsana madala zikowathuyu akupiti kuphophotsono likukhalangati lilibetsogoleli OK km ndilindichikhulupililo kut kulilakwathumwakuve ndithu ndikuziwakuti muchitapokathu

  4. Kodi sanali pa wailesi? Chifukwa atola nkhani amanama kwabasi.
    Anatiuza kuti Peter wafa, lero akukanira anthu kuti inali mphekesera ua m’chipatala. Anthu ake ati oposa atola nkhani?

  5. umbuli ndiumene ukutipha kodi mene munayambila kunyoza munja mwapindula chani agaru inu eeeee tamusieni muthu azipuna zake zinayeratu inu mukhalila yomweo yomanyozayo eeee alesi

  6. Amalawi dziwani kut boma lakangalika kupanga ma reformz so,,,kusowa kwa mankhwala + ndalama,,,kuvuta kwa magetsi + madzi & kukwela kwa mitengo ya katundu + kuchedwa kwa malipiro ndizipatso za”public reformz”

  7. From where I’m seating. ..it is 1:15pm. The count down continues. In 45 minutes I want to see my president speaking to journalists in robust health. I guess I will see him gesturing using his right hand and not his left only.

  8. Abwana awuzeni anthu kuti mukudwala,chifukwatu ndizochita kuwonekelatu nanga muzichita kubisa ngati mutodwala kanyela isiii!!!!

  9. Koma muli ndi mbiri vuto lanu chenicheni ndichani yoh yoh pangani zanu zimene zingakuthandizeni.mukulimbana ndi munthu woti ali ndi ndalama kale zake zinayera kale inu koma kukanda akalungu nsense.kunali muluzi analipo enaso ena amalimbana naye chifukwa chakuchita bwino kwake pano muluzi ali kuti????? Samalani abale polimbana ndi anthu andalama muzafa imfa yowawa

Comments are closed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading