21 October 2016 Last updated at: 11:40 AM

A Mutharika mwina ayankhula kwa a Malawi lero

Pataphulika mphekesera zoti mtsogoleri wa dziko lino anachedwa mu dziko la Amereka kamba koti anagonekedwa ku chipatala, mkuluyu ali ndi mwai otsitsa nkhani zimenezo lero mwa yekha.

Malingana ndi a kunyumba ya boma ku Lilongwe, mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika lero akhala akuyankhula ndi atolankhani.

A kunyumba ya boma ati a Mutharika alankhulana ndi a tolankhani lero zokhudza ulendo wake wa ku Amereka koamnso nkhani zina.

A kunyumba yaboma ati atolankhani oposera makumi anayi aonetsa kale chidwi chofuna kumva mtsogoleri wa dziko lino.

“A President akumana ndi atolankhani lachisanu, pa 21 Okotoba,” anatero mneneri wa a President a Mgeme Kalirani.

Anthu ambiri akhla tcheru kumva a Mutharika kamba koti atafika mdziko muno sanalankhulepo ngakhale liwu limodzi ndipo anli okanika kugwiritsa ntchito mkono wawo wa dzanja lamanja.

Atafika anthu amene anali ndi chikayiko kuti mdziko la Amereka mkuluyu amadwala, anavomeleza ataona mmene anakanikila kugwilitsa ntchito mkono wa kumanja.134 Comments On "A Mutharika mwina ayankhula kwa a Malawi lero"