Chichokereni mu nthaka ya dziko la Malawi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika pamodzi ndi omutsatira pa 16 September chaka chino kupita ku United states of America, Maso a amalawi ali tcheru kufuna kumuonanso atamusowa.
A Mutharika akuyenera kufika kuno kumudzi dziko limene amalitumikira lero lamulungu pa 16 Okotobala malinga ndi chikalata chochokera ku nyumba ya boma.

Kukhalitsa kwa mtsogoleli wa dzikoyu kudadzetsa mpungwepungwe pamene anthu ochuluka amafuna kudziwa za komwe iye ali ndi zomwe akuchita koma amalawi samakhutitsidwa ndi zomwe nduna yofalitsa nkhani a Malison Ndau amanena kuti a Mutharika akugwira ntchito zothandizira kutukula dziko la Malawi pomwe samatsindika za komwe iwo ali.
Anthu miyandamianda akhala ali tcheru maso awo pa khomo la ndege 1 koloko masana kuti awone mtsogoleri wawo yemwe anamusowa kwa nthawi yayitali atapita ku dziko la chilendo.
Kufika kwa a Mutharika, kukhala kokwanira kufufuta kotheratu mphekesera zonse zomwe anthu anali akukamba kuti sakupeza bwino m’thupi ndipo ali ku chipatala, enanso amati a Mutharika ali mwa kayakaya uko kumene anali.
Mtsogoleriyu adachoka kuno ku Malawi mwezi watha kupita ku msonkhano wa atsogoleri a mmaiko osiyanasiyana (United Nations General Assembly) ku America, koma adaonjezera masiku ake okhalira ku dziko la chilendo ngakhale masiku a msonkhano adali atatha kale.
Nawo atolankhani ali tcheru kudikira kuti awone ngati akanizidwe kudzakumana ndi a Mutharika kapena ayi pamene pamamveka kuti kufika kwa a Mutharika kudzakhala kouma ku nkhani ya uthenga pomwe “pakumveka kuti atolankhani sadzaloledwa kufusa mafunso mtsogoleri wa dzikoyu”
Koma a ku nyumba ya boma atsutsa manong’onong’owa, ponena kuti pulezidenti Mutharika ali okonzeka kulankhula ndi atolankhani.
357 thoughts on “Maso a amalawi ali tcheru ku bwalo la ndege la Kamuzu”
Comments are closed.


Koma asamazimitse phone koyenda mumuuze plz
Kodi Ali moyo?
Anabwela sanabwele
Pa chichewa pali mawu omati “mawu msamatha” tsanu onthu wena ongutha mawu koma dala sibwino ntha zina kuti ozanu okutameni. Galimoto imaphweka okamayendetsa wina onthuni.
Iwe Munthuyu Anayimika Mkono Umodzi Ndiye Ukutipatsira Ataimika Mikono Iwiri Bwanji? Nawe Wayamba Ziphuphu
Mesa wafika
God is great
Comment reserves
Mtsogoleri wadziko lino amwarilad inu simukuwona kuti akugwilitsa ntchito dzanja la madzele kkkk.
Kkkkk akapalamula mwayankhulatu si fisi wa satanism uja amamutchukitsa a koma akunama tilinayenaye pa 2019 pa ma vote ake tamusungila azapitilizatso kuwadyetsa atumbuka onse zitete kkkk pantumbo pa tumbuka.
mmmmmm kom sindikukhululira kut ndiyewmeyu ayi tiunseni bwino
ameneyu kuno sikawo ofunika apatsidwe 30 days muziko lathu lino,dziko la masiye lino atsogoleli amangopanga zomwe iwo akufuna, cz amalawi timapheledwa ufulu olankhula ,President akakhale dziko la eni mwenzi okwana ndithu ,osaopaso anthu amene anamuuika pa ,pampando
A Malawi opusa adyera komanso ankhanza.Mumafuna atafa kuti mubenso Ndalama zina. Mwalephera.HE is there til 2024 .
Mukakhuta madeya anuwo musamaelekezele nzanu kut wamwalira mutayambe ndinu iye aliphee mulungu ndyemwe azamutenge osat inu ayi
welcome back ambuye! we all love u!
Kwa amene mukunyoza ndinuzitsilu komaso wopandazelu ndiye mwapambana chani kubwelako?
May God bless our President,Long lives, Genuine Democrancy.
long live Muntharika
Satana nthawi zonse ndiwolephera, welcome Mr president, ife tili nanu, zikumuwawa akachite report ku police yomwe ali nawo pafupi,DPP chipani chawanthu.
Osat nama akuyimika mkono umodzi not mikono yonse