16 October 2016 Last updated at: 9:17 AM

Maso a amalawi ali tcheru ku bwalo la ndege la Kamuzu

Chichokereni mu nthaka ya dziko la Malawi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika pamodzi ndi omutsatira pa 16 September chaka chino kupita ku United states of America, Maso a amalawi ali tcheru kufuna kumuonanso atamusowa.

A Mutharika akuyenera kufika kuno kumudzi dziko limene amalitumikira lero lamulungu pa 16 Okotobala malinga ndi chikalata chochokera ku nyumba ya boma.

Peter Mutharika Ethiopia

President Mutharika fika lero.

Kukhalitsa kwa mtsogoleli wa dzikoyu kudadzetsa mpungwepungwe pamene anthu ochuluka amafuna kudziwa za komwe iye ali ndi zomwe akuchita koma amalawi samakhutitsidwa ndi zomwe nduna yofalitsa nkhani a Malison Ndau amanena kuti a Mutharika akugwira ntchito zothandizira kutukula dziko la Malawi pomwe samatsindika za komwe iwo ali.

Anthu miyandamianda akhala ali tcheru maso awo pa khomo la ndege 1 koloko masana kuti awone mtsogoleri wawo yemwe anamusowa kwa nthawi yayitali atapita ku dziko la chilendo.

Kufika kwa a Mutharika, kukhala kokwanira kufufuta kotheratu mphekesera zonse zomwe anthu anali akukamba kuti sakupeza bwino m’thupi ndipo ali ku chipatala, enanso amati a Mutharika ali mwa kayakaya uko kumene anali.

Mtsogoleriyu adachoka kuno ku Malawi mwezi watha kupita ku msonkhano wa atsogoleri a mmaiko osiyanasiyana (United Nations General Assembly) ku America, koma adaonjezera masiku ake okhalira ku dziko la chilendo ngakhale masiku a msonkhano adali atatha kale.

Nawo atolankhani ali tcheru kudikira kuti awone ngati akanizidwe kudzakumana ndi a Mutharika kapena ayi pamene pamamveka kuti kufika kwa a Mutharika kudzakhala kouma ku nkhani ya uthenga pomwe “pakumveka kuti atolankhani sadzaloledwa kufusa mafunso mtsogoleri wa dzikoyu”

Koma a ku nyumba ya boma atsutsa manong’onong’owa, ponena kuti pulezidenti Mutharika ali okonzeka kulankhula ndi atolankhani.359 Comments On "Maso a amalawi ali tcheru ku bwalo la ndege la Kamuzu"