11 October 2016 Last updated at: 8:46 PM

A Mutharika akubwera la Mulungu

Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika amene anakomedwa mu dziko la Amereka alengeza tsopano kuti afika kuno ku Malawi lamulungu masana.

Malingana ndi chikalata cha kunyumba ya boma, a Mutharika amene anapita ku dziko la Amereka sabata zitatu zapitazo akhala akubwelela ndipo adzafika mu dziko lino masana nthawi ikazakwana 1 koloko.

Peter Mutharika

Peter Mutharika akubwera sabata lino.

“President Mutharika akhala akufika amu dziko lino atakhala nao pa msonkhano wa mayiko onse, wa United Nations, komanso atagwila nawo ntchito zina za boma,” atero a ku nyumba yaboma.

Kuyambila sabata latha, nkhani zinatchuka zoti mtsogoleri wa dziko linoyi wagwidwa ndi matenda ku dziko la Amereka ndipo ali ku chipatala komwe ali mwa kayakaya.

Koma a kunyumba ya boma anatsutsa izi ndipo ananena kuti Mutharika adakali wangwiro ndi wamphamvu.

A boma anachenjeza kuti aliyense onena kuti a Mutharika ali pang’ono kufa anjatidwa ndipo akagwila ukaidi. Izi zinapangitsa mangong’onong’o onena kuti mtsogoleriyu sakupeza bwino kupita patali ndipo ena anonjeza kunena kuti a Mutharika basi apitilila.548 Comments On "A Mutharika akubwera la Mulungu"