10 October 2016 Last updated at: 11:01 AM

Onse onena kuti Mutharika wamwalira kapena akudwala amangidwa

Ndende ikudikila anthu onse amene akufalitsa nkhani yoti mtsogoleri wa dziko lino, a Peter Mutharika, akudwala mwakayakaya mu dziko la Amereka.

Malingana ndi nduna yofalitsa nkhani imenenso ili mneneri wa boma, mtsogoleri wa dziko lino’yi amene anapita ku dziko la Amereka ku msonkhano waukulu wa maiko onse ali bwino ndipo ndi wathanzi.

Izi zi kusiyana ndi malipoti ena amene anatchuka oti a Mutharika akuonela pakhosi ndipo tsiku lina lilironse anthu atha kulandila uthenga wa chisoni.

Peter Mutharika

Peter Mutharika pofika ku America.

A boma anenetsa kuti a Mutharika sali mwa kayakaya ndipo anthu onse otchukitsa zimenezo ndi ana a Satana chabe amene amadya bodza.

“Nkhani zoti a Mutharika akudwala ndi bodza la mkunkhuniza, zilubwe ndipo ndi bodza lochititsa nseru kwabasi,” afotokoza chotelo a Ndau mu kalata imene alemba yopita ka mtundu wa a Malawi.

“Tikufuna tikumbutse a Malawi kuti ife a boma tinanena kale kuti a Mutharika akugwila ntchito zina ku dziko la Amereka,” apitiliza motelo a Ndau.

A Ndau aonjezelapo kuchenjeza anthu onse kuti boma silinyengelela koma kutengela ku khoti a kapilikoni onse amene akutchukitsa zoti mtsogoleri wa dziko lino watsala madzi amodzi ati poti uwu ndi mlandu malingana ndi malamulo a dziko la Malawi.

“Kutchukitsa nkhani ya bodza yokhudzana ndi umoyo wa mtsogoleri wa dziko ndi mlandu waukulu oti munthu amayenela kumangidwa nawo,” atero a Ndau.741 Comments On "Onse onena kuti Mutharika wamwalira kapena akudwala amangidwa"