20 September 2016 Last updated at: 10:45 AM

Anthu okana kuti kuli Mulungu achita msonkhano, anyadila poti chiwelengelo chawo chikukula

Bungwe la anthu okana ndi okayika kuti kuli Mulungu kunja kuno, la Association of Secular Humanists (ASH), la ku Malawi kuno linachita msonkhano wawo wa pa chaka pachiwelu mu mzinda wa Lilongwe.

Cholinga cha msonkhanowu chinali chofuna kudziwana kuti alipo angati amene akuletsa zoti kuli Mulungu ku Malawi kuno komanso kuchitilatu ndondomeko ya zinthu zomwe akufuna kuchita mu zaka zikubwelazi.

Malingana ndi mmodzi mwa anthu amene amakana kwa m’tu wagalu kuti kuli Mulungu kunja kuno a George Thindwa, bungwe lawo ndi lokondwa kuti tsopano anthu ambiri ayamba kuzindikila kuti kukhulupilila Mulungu ndi kutaya nthawi.

george thindwa

Thindwa adasogolera anthuwa.

“Chiwelengelo chathu chikukula, ndipo iyi ndi nkhani yabwino,” anatero a Thindwa amene ndi munthu otchuka kwambiri pa nkhani yokana kuti kuli Mulungu.

Iwo anaonetsanso kukondwa kawo Kamba koti achinyamata ambiri akuzindikila kuti kuli bwino kusakhulupilila Mulungu, bola kuzikhulupilila mwa umwini okha.

“Pakubwela achinyamata ambiri, iyi ndi nkhani yabwino. Dziko lino likupita kotukuka ndithu ngati achinyamata athu angazindikile kuti kulibe Mulungu,” iwo ananyadila motero.

Bungwe la ASH limalimbikitsa kukhulupilila mwa munthu ndipo limanena kuti dziko silizatha, ufiti kulibe ndiponso nkhani ya Mulungu ndi nthano chabe.886 Comments On "Anthu okana kuti kuli Mulungu achita msonkhano, anyadila poti chiwelengelo chawo chikukula"