15 September 2016 Last updated at: 11:55 AM

A Kaliati agwila a Nankhumwa ufiti

Ziwanda zandeu zinabisala kuchipani chotsutsa cha Kongeresi chija tsopano zavumbuluka ndikupita ku chipani cholamula.

Malingana ndiu thengaumene ukufalitsidwa, nduna yoona zama boma aang’ono a Kondwani Nankhumwa ili ndivuto loti ikumankakunena mabodza nduna zimzake ndicholinga choti akome kwa President Peter Mutharika.

Uthengawu umene ukuoneka kuti unajambulidwa ndi Mayi Patricia Kaliati, amene ndinduna yoona zophunzitsa anthu, ulindi munthu wina okonda MayiKaliati amene wawayimbila phone kuti awachenjeze kuti asamale pocheza ndi Nankhumwa chifukwa mkuluyu ndinjoka mu udzu.

“Akufunaudindowanu,” mkuluwina akuchenjeza Mayi Kaliati amene akungokhala kumamvela. “Ndalamazimenemumalandilangatindunamukayendapaulendozimamupweteka.”

Uthengawu ukumveka kuti unajambulidwa nthawi imene Mayi Kaliati anali induna yoona zofalitsa nkhani ndipo anali pamseu pafupifupi tsikuli lilonse ukuakumapatsidwa makobili aja amatchedwa ma alawansi.

Mkulu amene akuchenjeza a Kaliati akuwauza kuti bamboo Nankhumwa ali pa kalikiliki kuphamika phula a President ndicholinga apeze udindo umene tsopano wapitakwa a Malison Ndau.161 Comments On "A Kaliati agwila a Nankhumwa ufiti"