Nonse okonda kutukwana chenjerani: zaka zisanu kundende mukapezeka mukutukwana

Advertisement
Maula prison

Palibe kutsuka mkamwa mwachikunja, mukatero mukapezeka kujere ndi kugwira ya kalavula gaga.

Mkulu wina ku Ntchisi amulamula kukakhala ku ndende kwa zaka zisanu pa chifukwa chotukwana mayi wake ndi kutchula ziwalo zobisika.

Maula prison
Wa ku Maula kamba kotukwana

Malingana ndi bwalo lalin’gono la mu boma la Ntchisi, a Pilirani Banda omwe ndi a zaka 27, akuyenera kukakhala kundende chifukwa anatukwana koopsa mayi wawo.

Bwaloli linamva kuti pa 2 August chaka chomwe chino, a Banda anapsetsana mtima ndi mayi wawo. Anasinthana Chichewa chosakhala bwino ndipo a Banda anakwiya kwambiri ndi kuyamba kutukwana mayi wawo chikunja, kutchula ziwalo zobisika za mayi wawo ndi kuwaopseza kuti awapweteka ku malo obisikawo.

A Banda atafunsidwa za mlandu uwu iwo anauvomela.

Woweluza milandu pa bwaloli, Yohane Nkhata, sanachedwe koma kuwagamula a Banda kuti apite ku ndende akagwile ukaidi wa kalavula gaga kwa zaka zisanu.

A Banda anagamulidwa chotere pa chifukwa chogwilitsa mau otukwana amene anali ndi cholinga chofuna kupsetsa mtima munthu ndi kumupangitsa kuti apalamule mlandu.

A Malawi ambiri saona cholakwika ndi kutukwana maka achinyamata a mu sukulu za ukachenjede amene akakwera basi zawo amatulutsa mitu pa windo ndi kumatukwana anthu. Mwina posachedwa nawo amangidwa.