Kasambara agamulidwa: akasewenze ya kalavula gaga kwa zaka khumi ndi zitatu
Bwalo la milandu lalikulu mu mzinda wa Lilongwe dzulo lachiwiri pa 30 August lalamula nduna yakale yoona za malamulo a Ralph Kasambara kuti akagwire ukaidi wa kalavula gagag kwa zaka khumbi ndi mphambu zitatu.
A Kasambara anapezeka olakwa pa mlandu okonza upo ofuna kupha a Paul Mphwiyo mu chaka cha 2013.
Malingana ndi oweruza mlandu wa bwaloli a Justice Micheal Mtambo, a Kasambara akuyenela kukasewenza kwa nthawi yochuluka chonchi kamba koti mlandu umene anapezeka olakwa ndi waukulu. Oweruza mlanduyu ananenanso kuti a Kasambara apatsidwa chilango chokhwima chonchi Kamba koti anaonetsa kusaweruzika mu nyengo imene amaimbidwa mlandu.

“Inu ndi munthu oipa mtima kwambiri,” oweruza mlandu anadzudzula choncho a Kasambara. “Nthawi yonse yomwe mumaimbidwa mlandu munaonetsa khalidwe ngati mbuli yosazindikila ngakhale muli munthu odziwa malamulo wamkulu.
“Inu munalankhula zinthu zoti sizimayenela kulankhulidwa mu bwalo la milandu ndipo munakhala mukuopseza anthu. Inu simunasonyeze chisoni kapena kuzichepetsa mu nthawi yonse yoimbidwa mlandu,” anatero Mtambo.
Oimira mlandu a Kasambara amapempha bwalo kuti liwamvele chisoni ndi kuwapatsa ka chilango kochepa ati poti a Kasambara ndi mkulu amene wathandiza dziko lino ngati mkulu wa za malamulo komanso nduna yaboma, iwo anaonjezelapo kunena kuti a Kasambara ndi munthu wa chichepele amene angathe kuthandiza dziko lino.
Zonse anakambazi sizinaphule kanthu pamene a bwalo analimbira mtima a Kasambara ndi kuwatumiza kundende kwa zilumika khumi ndi zitatu.
Ena amene anapezeka olakwa pamodzi ndi a Kasambara ndi a Pika Manondo ndi a MacDonald Kumwembe. Awiliwa awakwapula ndi zaka makumi awiri kuonjezerapo mphambu zisanu ndi imodzi aliyense pa mlandu ofuna kupha a Mphwiyo komanso okonza upo ofuna kupha a Mphwiyo.
Latest vacancies
64 thoughts on “Kasambara agamulidwa: akasewenze ya kalavula gaga kwa zaka khumi ndi zitatu”
Comments are closed.









Sticker ili pa jeketeyo yachipani chanji?
Kodi walakwa chani
ABAKHA OPANDA AMBUYAwO AMENEWO.
http://mdubvibe.com/song-details/?sid=9904
àbale anga choñdechonde tiyeni musandisiye ñdekha ukwati wanga ndiwammawa ndimkadzi wamalemu kansambala
#bambo kasambala* ndikufunilani kulavulagaga kwabwino ndagovakumene KUTI ng’ombezatembeka kuyana kudazibomo sindikuwakuti mmenezimatele masexchoni anu analikuto monga mkuluwama sexchoni eeeee APA zikungooneselatu KUTI paribe wapambana lamulo ndavomeleza kanene Ku Zambia nanutso tumakasamba tatin’gonotin’gono mutengelepo phuzilo the end went ,,,,,comment lodng tauch angen to sev
Ngati umayenda mbali siku ndilimoZi limakwana
Zaka Zachepa.Amatonjeza Agal Amenewa.
Wachuma siwosela nayo anhkala ngati ali kunyumba kwawo amenewo kalavula gaga amangwira woba mbuzi
Rapha ndi dolo
Mbava iyi zausilu
That’s not fair munthuyu sadalakwe
Tienazon
akuba nokha nokha inu mungofuna kutipusitsa bas mumacheza limodzi kumbaliko zankutu bas mapaz anu nose
mmm kkkkkkkkkkkkk!!!!
Lamulo liposa mphavu
amaziona ngati ndi doro lero ndizi wasanduka Dorophe!
alii kundende ,,, komanso azidya bhoo kuposa maa prison guards,,, ukuxiwakale ndizoti ndi #Rich_Nigger
Ndende ilibenso kut ukudya bwino..mayaz….as long as ali mu cage..bas…anva kuwawa…..kukhala pa wekha No!! Dona muthu wabanj its not a joke..
Basi aseweze.samaiziwa ndende afuse ife!
Kkkkkkk zili bwino apa ndiye timati galu waluma mbuyake.