29 August 2016 Last updated at: 10:05 AM

Musaletse mowa; a Malawi akwiya ndi malingaliro ofuna kuletsa mowa

Gulu la a Malawi okonda chakumwa lakwiya koopsa ndi malingaliro omwe mabungwe ena kaunena oti pakufunika malamulo oletsa a Malawi kumwa mowa pa nyengo zina.

Pothilira ndemanga pa nkhani yomwe ife a Malawi24 tinalemba yoti bungwe lina lomwe si la boma la Drug Fight Malawi likupempha boma kuti lichite machawi kuvomeleza ndondomeko yoona za kamwede kamowa yomwe pachingelezi ikutchedwa National Alcohol Policy, a Malawi anasonyeza kuti ndi osakondwa kuti anthu ena akufuna pakhale malamulo a padera oona za kamwedwe ka mowa.

“Linotu si dziko la chipembedzo chinachake, musayese ndi la Chislamu kapena Chikhristu. Tisiyeni tizipyoza mowa wathu,” wina analemba monyangala.

Beer

Mowa usaletsedwe ku Malawi.

“Aaah mukufuna mudziko muno mukhale anthu ochepatu chifukwa tonse a mowa tisamukila ku mayiko amene kuli mowa,” wina anaopseza motelo.

Wina popowa kulankhula zambiri, anangonena kuti: “zopusa zimenezo!”

Koma mkulu wa bungwe la Drug Fight Malawi amene akutsogolera mabungwe amene akufuna kuti pakhale malamulo okhwima pakamwedwe ka mowa, a Nelson Zakeyu ananena kuti cholinga chawo ndi chakuti boma liteteze anthu ku mowa, makamaka a chichepere.

“Boma likuyenela kuvomeleza ndondomeko zatsopano izi zomwe zikukhudzana ndi kamwede, kagulitsidwe ndi kapezekedwe ka mowa. Cholinga chake ndi choti titeteze anthu ku mowa, makamaka achinyamata amene akuonongedwa ndi mowa,” anatero a Zakeyu.

Koma mawu awo sikuti akondweletsa a Malawi amene akuoneka kuti amakonda chokumwa chawo moopsa.272 Comments On "Musaletse mowa; a Malawi akwiya ndi malingaliro ofuna kuletsa mowa"