Yathela ma penalty: wa njuga wachitidwa njuga ndi malume ake

Advertisement

…52 miliyoni yanga ya bet yapita

Zija ankapanga azimalume kalekale zomakunyengelera chimanga chophika kuti akonze nsewu zamuonekera James Chaola amene anawina bet ya 52 miliyoni. Kusiyana kwake ndi koti iye sanamubwenzere ndi komwe chenje, amuuza kuti akasume kumene akufuna.

Malipoti ochokera pa tsamba la Mikozi akuonetsa kuti mnyamata amene anapambana njuga wachitidwa njuga imene ndi a malume ake.

Malinga ndi Chaola, iye anapambana njugayi kumayambiliro kwa chaka chino. Kampani ya njuga ya Premier Bet inamupatsa cheke cha 52 miliyoni.

Chaola ndi ophunzira pa sukulu ya Maranatha ndipo wati iye sanaganizeko zosiya sukulu kuti akadyelere ndalama. Amafuna asakanize u mpondamatiki ndi sukulu. Pa chifukwa ichi, anayika ndalamazi ku akaunti ya a malume ake.

“Sizikanatheka kuti nditenge ndalama zonse ndipite nazo ku Nsanje,” anafotokoza Chaola amene akuti amakhala ndi Mayi ake ku Nsanje. Iye anaonjezerapo kuti asananyamuke kupita ku sukulu anafotokoza kwa malume ake dongosolo limene anapanga lakagwiritsidwe ntchito ka ndalama.

“Ndimafuna ndimangire nyumba Mayi wanga, nditumize abale anga ku sukulu, ndipo ina ndikanathandiza malume anga ena kuti bizinesi yawo ikule,” anatero Chaola.

Iye wati anapita ku sukulu ndi mtima wa chisangalaro kukhulupilira kuti maloto ake akwanilitsidwa mmbuyo muno. Koma tsoka ndi ilo, Freddy anatulukira ndi kugwetsa msasa umene Mayi wake ndi abale ake amakhalapo. Iwo anathawira ku camp.

Nyengo itapola moto, Chaola wati anafunsa malume ake kuti amupatse ndalama amasunga zija ndi cholinga choti ayambe kumanga nyumba ya Mayi wake. Apo ndi pamene adadziwa chifukwa chimene akulu akale adapanga mwambi woti mwana wa mzako ndi wako yemwe, ukachenjera manja udya naye.

“Anandifunsa kuti ndalama zake ziti?” wadandaula Chaola. “Ndipo nditachititsana nawo makani anandikumbutsa kuti ndalama ndidawapatsa ndekha. Sanachite kundibera ayi.”

Pakali pano, Chaola wati akufuna anthu akufuna kwabwino amuthandize ndi njira zokakamiza malume ake kuti amubwenzere ndalama zake.

Advertisement